Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

APRIL 22, 2014
RUSSIA

Anthu Ena a ku Russia Akuimbidwa Mlandu Chifukwa cha Chikhulupiriro Chawo

Anthu Ena a ku Russia Akuimbidwa Mlandu Chifukwa cha Chikhulupiriro Chawo

Anthu 16 a Mboni za Yehova a m’dera la Taganrog ku Russia akuimbidwa mlandu chifukwa chosonkhana kuti alambire Mulungu mwamtendere. b Aka n’koyamba kuti a Mboniwa azengedwe mlandu ngati umenewu. A Mboniwa akapezeka kuti ndi olakwa, ndiye kuti akhoza kulipitsidwa chindapusa cha ndalama mpaka zokwana marubozi 300,000 (madola 10,000) aliyense, kapenanso akhoza kuikidwa m’ndende mpaka kwa zaka 8. A Mboni 16 amenewa alamulidwa kuti asachoke ku Taganrog mpaka khoti litapereka chigamulo pa nkhaniyi.

Anthu a Mboni za Yehova anayamba kuzunzidwa m’dera la Taganrog mu June 2008. Zimenezi zinayamba kuchitika pamene mkulu woimira boma pa milandu anadula chisamani kukhoti lalikulu ku Rostov, n’cholinga chothetsa bungwe la a Mboni za Yehova la m’derali. Mkuluyu ananenanso kuti m’mabuku a Mboni za Yehova mumapezeka mawu oopsa. Khotili linagamula mlanduwu mokomera boma, ndipo pa December 8, 2009, khoti lalikulu kwambiri la m’dzikolo linagwirizananso ndi chigamulochi.

Zimene linachita khoti lalikululi zinachititsa kuti akuluakulu a boma a m’dera la Taganrog alande Nyumba ya Ufumu (nyumba yolambiriramo) ya Mboni za Yehova ya m’derali. Choncho anthu a Mboniwa anayamba kusonkhana m’nyumba za anthu polambira Mulungu. Khotili linagamulanso kuti akuluakulu aboma la Russia aike mabuku 34 a Mboni za Yehova pam’ndandanda wa mabuku oopsa omwe ndi oletsedwa m’dzikolo. Komabe a Mboni za Yehovawo akuyesetsa kumenyera ufulu wawo wolambira, moti adandaula ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya.

Zimene makhoti anagamula zinachititsa kuti akuluakulu a boma m’dera la Taganrog, apezerepo mpata wovutitsa ndiponso kuchitira nkhanza a Mboni. Mu 2011, apolisi anayamba kufufuza m’nyumba za anthu a Mboni zokwana 19, ndipo nthawi zina ankayamba kufufuzaku 6:00 m’mawa. Akalowa m’nyumba ankadzutsa aliyense, kaya ndi mwana kapena wachikulire. Apolisiwa ankafufuza mabuku omwe amawaganizira kuti ndi oopsa ndipo ntchitoyi inkatenga maola 8 mpaka 11. Iwo ankalanda mabuku onse a chipembedzo pamodzi ndi katundu wa anthu a Mboniwo. Kuwonjezera pamenepa, akuluakulu a boma ankajambula mavidiyo mwachinsinsi, a misonkhano ya a Mboni n’cholinga choti aimbe milandu anthu omwe anasonkhana. Zimene zikuchitika ku Taganrog zachititsa kuti boma liyambenso kuchitira nkhanza a Mboni m’dziko lonse la Russia. c

A Mboni za Yehova ndi gulu lodziwika bwino padziko lonse. Malamulo a dziko la Russia ndiponso mfundo za mu Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya, zimasonyeza kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wolambira. Ndipo makhoti akuluakulu padziko lonse amavomereza kuti munthu aliyense, kuphatikizapo wa Mboni za Yehova, ali ndi ufulu umenewu. Ndiye n’zodabwitsa kuti akuluakulu a boma m’dera la Taganrog, akuchita zinthu ngati kuti a Mboni alibe ufulu umenewu.

Mlanduwu upitirirabe mpaka mwezi wa May, pamene khoti lidzapereke chigamulo litamva madandaulo a mbali zonse. Ngati khoti lidzagamule kuti anthu 16 a Mboni aja ndi olakwa, ndiye kuti zimenezi zidzakhudza ufulu wa a Mboni ena oposa 800, omwe ali m’dera la Taganrog. Ndiponso zidzachititsa kuti anthu a Mboni amene ali ndi milandu kukhoti m’madera ena ku Russia, zinthu zisadzawayendere bwino.

Bambo Grigory Martynov, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Russia, ananena kuti: “N’zosaloleka kuti misonkhano yathu izisokonezedwa. A Mboni za Yehova si anthu oopsa ndipo sangasokoneze mtendere m’dziko la Russia. Koma akuluakulu a boma akungotichitira nkhanza chifukwa chakuti ndife Mboni za Yehova basi.”

a Chithunzichi chikungosonyeza anthu 10 okha pa anthu 16 amene akuzengedwa milandu.

b M’chaka cha 2012, akuluakulu a boma la Russia anayamba kuimba mlandu anthu 16 a Mboni ponena kuti aphwanya Gawo 282.2(1) ndi (2) la malamulo a dzikolo. Ngati anthuwa atapezeka kuti aphwanyadi lamuloli, ndiye kuti akhoza kuikidwa m’ndende mpaka zaka zitatu. Anthu 4 pagululi ndi akulu mumpingo wa Mboni za Yehova, ndipo akuwaimbanso mlandu wophwanya Gawo 150(4) la malamulo a dzikolo. Ngati angapezeke kuti ndi olakwa, ndiye kuti akhoza kuikidwa m’ndende kwa zaka 5 mpaka 8.

c Kungoyambira pa December 8, 2009, pamene khoti lalikulu kwambiri linagwirizana ndi chigamulo cha khoti lalikulu ku Rostov, apolisi amanga anthu a Mboni 1,600, ndiponso kuletsa mabuku awo okwana 70 omwe akuwatchula kuti ndi oopsa. Apolisiwa anafufuzanso m’nyumba za anthu a Mboni pamodzi ndi malo awo olambirira, zokwana 171, ndipo analetsa kapena kusokoneza misonkhano yokwana 69.