Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JULY 31, 2014
RUSSIA

Khoti la ku Taganrog Lapeza a Mboni za Yehova Kuti ndi Olakwa Chifukwa Chochita Zinthu Zokhudzana ndi Chipembedzo Chawo

Khoti la ku Taganrog Lapeza a Mboni za Yehova Kuti ndi Olakwa Chifukwa Chochita Zinthu Zokhudzana ndi Chipembedzo Chawo

Pa July 30, 2014, khoti la munzinda wa Taganrog linagamula kuti anthu 7 mwa anthu 16 a Mboni a mumzindawu omwe amaimbidwa mlandu ndi olakwa chifukwa chokonza ndiponso kuchita misonkhano ya chipembedzo chawo mwamtendere. A Mboniwa anagamulidwa kuti ndi olakwa chifukwa cholambira Mulungu monga mmene a Mboni anzawo amachitira padziko lonse lapansi. Izitu zikuonetseratu kuti ufulu wolambira wa a Mboni za Yehova m’dziko lonse la Russia uli pangozi.

Woweruza milandu anakonza zoti adzawerenge chigamulo cha mlanduwu pa July 28, 2014, koma anasintha ndipo anawerenga mawa lake. Choncho pa July 29 woweruza milanduyo anayamba kuwerenga chigamulo cha masamba 100 chomwe chinatenga tsiku lonse mpaka m’mawa wa tsiku lotsatira pa July 30. Woweruzayo anagamula kuti azibambo 4 a Mboni omwe ndi akulu mumpingo, akakhale ku ndende, ena kwa zaka 5 ndipo ena zaka 5 ndi hafu komanso kuti alipire chindapusa cha ndalama zokwana marubozi 100,000 (madola 2,800 a ku America.) Kenako a Mboni ena atatu anagamulidwa kuti alipire chindapusa cha ndalama zokwana marubozi pakati pa 50, 000 ndi 60,000 aliyense (madola pakati pa 1,400 ndi 1,700 a ku America.) Koma woweruzayo ananena kuti a Mboniwo asapereke ndalama za chindapusazo chifukwa chakuti kufufuza mlanduwu kwatenga nthawi yaitali zomwe n’zosemphana ndi malamulo ndipo ananenanso kuti a Mboniwa sapita kundende nthawi yomweyo. Ndiyeno a Mboni 9 enawo anapezeka kuti ndi osalakwa.

Woweruzayo anagamula mlanduwu potengera zimene khoti la ku Rostov linagamula mu 2009 pa mlandu winanso wokhudza a Mboni, pofuna kuthetsa chipembedzo cha a Mboni ku Taganrog. Ngakhale kuti chigamulo cha 2009 chinali chokhudza kuthetsa bungwe loimira a Mboni, woweruzayo ananena kuti chigamulo chomwe iye anapereka chikuletsa zochita zachipembedzo zonse za a Mboni za Yehova ku Taganrog komanso m’madera ozungulira mzindawu.

Pa miyezi 15 imene mlanduwu unkazengedwa, a Mboni amene ankaimbidwa mlanduwa ananenetsa kuti sasiya kutsatira zimene amakhulupirira ndipo apitirizabe kulambira Mulungu monga a Mboni za Yehova. A Mboni omwe apezeka kuti ndi olakwa pa mlanduwu ali pa ngozi yoti akhoza kumangidwa ngati atapezeka kuti akuchita zinthu zokhudza chipembedzo chawo zomwe aletsedwa.

Bambo Victor Zhenkov, omwe anali m’modzi wa maloya oimira a Mboni pa mlanduwu anati: “Ndikuda nkhawa ndi zomwe zingachitikire a Mboni kuno ku Russia chifukwa cha chigamulochi. Pali nkhawa yakuti akuluakulu a boma angayambe kugwiritsa ntchito zomwe khotili lagamula pofuna kuipitsa mbiri ya a Mboni n’cholinga choti aziwazunza ndiponso kuwamanga akamachita zinthu zokhudzana ndi chikhulupiriro chawo.”

A Mboni za Yehova achita apilo chigamulochi ku khoti lalikulu la ku Rostov.