JUNE 2, 2014
RUSSIA
Mlandu Wokhudza Anthu Ena a Mboni za Yehova Mumzinda wa Taganrog ku Russia Ukupitirirabe
Anthu 16 a Mboni za Yehova akhala akuimbidwa mlandu ku khoti lina mumzinda wa Taganrog, mpaka m’mwezi wa May 2014. Umenewu ndi mlandu woyamba m’dziko la Russia kuti anthu azikakamizidwa kusiya zimene amakhulupirira powazenga milandu. Munthu wina yemwe ali m’gulu la anthu amene akuimbidwa mlanduwu anati: “Sakufuna kuti ndizichita zosiyana ndi ena. Komanso sakufuna kuti ndiziuza ena uthenga wa m’Baibulo. Sindikudziwa kuti zitha bwanji.”
Akuluakulu a boma la Russia akupotoza dala malamulo adzikoli oletsa chinthu chilichonse choopsa. Kuyambira mu 2009, akuluakuluwa akhala akuchitira nkhanza kwambiri anthu a Mboni za Yehova pofuna kuwasokoneza kuti asamalambire Mulungu momasuka. Bambo Victor Zhenkov omwe ndi loya amene akuimira a Mboni za Yehova pa mlanduwu anati: “Ndakhala ndikuunika milandu yomwe a Mboni za Yehova akhala akuimbidwa pa zaka zapitazi ndipo ndaona kuti akuluakulu a boma akungodana ndi a Mboniwa.” Akuluakulu a boma m’dera la Taganrog akuchitira nkhanza kwambiri anthu a Mboni za Yehova ndipo zikungokhala ngati chipembedzo cha Mboni n’choletsedwa m’derali, ngakhale kuti a Mboni analembetsa chipembedzo chawo ku boma la Russia m’chaka cha 1992. Zimene akufuna akuluakulu a boma a m’dera la Taganrog n’zodziwikiratu. Wa Mboni winanso yemwe akuimbidwa mlanduwu anati: “Munthu wina wofufuza milandu ananena mosapita m’mbali kuti: ‘Ukangosaina pepala loti wasiya chipembedzo cha Mboni za Yehova, basi mlanduwu watha, sitikuvutitsanso ndipo uzipita kwanu.’”
Oweruza a khotili akhoza kugamula kuti anthu 16 a Mboni amene akuimbidwa mlanduwa ndi olakwa. Izi zingachititse kuti alipitsidwe chindapusa, agwiritsidwe ntchito mowakakamiza kapenanso aikidwe m’ndende. Ngati khoti lingapereke chigamulo chimenechi ndiye kuti anthu sakhalanso ndi ufulu wolambira Mulungu momasuka m’dziko lonse la Russia. Anthu onse a Mboni m’dzikoli adzakhudzidwa chifukwa nawonso akhoza kuimbidwa mlandu ngati atapezeka akulambira Mulungu. Mayi Alyona Borodina, omwe ndi loya winanso amene akuimira a Mboni za Yehova pa mlanduwu anati: “Akuluakulu a boma akuvutitsa kwambiri a Mboni za Yehova. Mabuku a Mboni akuikidwa m’gulu la zinthu zoopsa. Ngati khoti lingagumule kuti buku linalake ndi loopsa, ndiye kuti lingawonongedwe potsatira chigamulo cha khotilo. Munthu wina wolemba mabuku anati: ‘Ngati angayambe kuwotcha mabuku ndiye angayambenso kuwotcha anthu.’ Apa zikuonekeratu kuti akuluakulu a boma la Russia akusokoneza kwambiri ufulu wolambira.”
Pali chiyembekezo chakuti woweruza milandu adzapereka chigamulo chomaliza pa nkhaniyi m’mwezi wa June 2014. Anthu a Mboni za Yehova padziko lonse lapansi komanso anthu ena omwe amalimbikitsa ufulu wolambira ali ndi chidwi ndi zomwe khoti ligamule.