Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

DECEMBER 2, 2015
RUSSIA

Khoti la ku Taganrog Lagamula kuti a Mboni za Yehova 16 Ndi Olakwa Chifukwa Chochita Zachipembedzo

Khoti la ku Taganrog Lagamula kuti a Mboni za Yehova 16 Ndi Olakwa Chifukwa Chochita Zachipembedzo

Khoti la mumzinda wa Taganrog linapeza kuti a Mboni 16 amenewa ndi olakwa pa mlandu wokonza ndi kupita kumisonkhano yachipembedzo. Mlanduwu unkazengedwa kachiwiri ndipo unakhala kukhotili kwa miyezi 11. Khotilo linagamula mlanduwu potsatira lamulo loletsa anthu kukonza ndi kuchita zinthu zoopsa zomwe zingabweretse chisokonezo. Izi zinatheka chifukwa chakuti mu 2009 khoti lomweli linali litagwiritsa ntchito kale molakwika lamulo la dziko la Russia lokhudza zinthu zoopsa. a

Pa 30 November 2015, woweruza wina dzina lake A. V. Vasyutchenko anagamula kuti anthu 4 mwa a Mboniwa akhale kundende kwa zaka zoposa 5 chifukwa chokonza misonkhano yachipembedzo. Aliyense anamulipiritsanso ndalama zokwana madola 1,511 a ku United States. Woweruzayo analipiritsanso ena mwa anthu 12 otsalawo ndalama zokwana madola 300 ndipo ena madola okwana 1,050. Koma kenako woweruzayo ananena kuti anthuwo sayenera kulipira ndalamazo ndipo anthu 4 aja sakuyenera kupita kundende pa nthawiyo. Panopa sizikudziwika ngati anthuwo adzapitedi kundende pa nthawi ina kapena ayi. Komabe anthu onsewa anaweruzidwa kuti ndi olakwa.

Ayenera Kusankha Ngati Akufuna Kupitiriza Kuchita Zachipembedzo

A Mboni oposa 800 amene amakhala ku Taganrog akudera nkhawa zimene zingachitike chifukwa chosonkhana mwamtendere n’kumakambirana za m’Baibulo ndiponso kupemphera. A Mboni onse 16 aja anauza khoti kuti apitiriza kuchita zinthu monga a Mboni za Yehova. Koma popeza khotilo linagamula kuti ndi olakwa, chikhulupiriro chawo chikhoza kuyesedwa. Wa Mboni wina dzina lake Aleksandr Skvortsov anati: “Zinali ngati khotilo linatiuza kuti, ‘Ngati simusiya chikhulupiriro chanucho, mukhala akabwerebwere moti mupatsidwa chilango chokhwima.’”

A Mboni akumadera ena a ku Russia alinso ndi nkhawa chifukwa cha chigamulochi. Makhoti a ku Samara ndi ku Abinsk anagwiritsanso ntchito molakwika lamulo loletsa zinthu zoopsa. Makhotiwa anagamula kuti a Mboni, omwe amapembedza mwamtendere, akuswa lamuloli ndipo anathetsa bungwe la Mboni la m’maderawa. Akuluakulu a boma ku Russia akapitiriza kugwiritsa ntchito lamuloli molakwika, ndiye kuti a Mboni za Yehova apitiriza kuphwanyiridwa ufulu wawo wopembedza.

Akupitiriza Kumenyera Ufulu Wawo Wachipembedzo

Chigamulo cha khoti la ku Taganrog chikusonyeza kuti akuluakulu a boma la Russia akuyesetsa kuti athetse chipembedzo cha Mboni za Yehova. Chaka chathachi, akuluakuluwo anagamula kuti mabungwe awiri a Mboni amachita zinthu zoopsa zomwe zingabweretse chisokonezo. Kuyambira mu March 2015, akuluakulu a boma akhala akuletsa a Mboni kuti aitanitse Mabaibulo komanso mabuku ofotokoza Baibulo kuchokera kumayiko ena. Mu July, dziko la Russia linaletsa webusaiti ya Mboni za Yehova ya jw.org ndipo ndi dziko lokhalo limene linachita zimenezi. A Mboni anachita apilo zigamulozi kumakhoti ena a ku Russia. Anakasumanso milandu 28 ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya n’cholinga choti dziko la Russia lisiye kuwaphwanyira ufulu wopembedza.

A Mboni 16 a ku Taganrog aja akuganiza zochita apilo chigamulocho n’kupitiriza kumenyera ufulu wawo. Woimira ofesi ya Mboni za Yehova ku Russia dzina lake Yaroslav Sivulskiy anati: “A Mboniwo akhala akuyankha mlanduwu kukhoti kwa zaka zoposa ziwiri ndi hafu. N’zomvetsa chisoni kuti ayenera kupitanso kukhoti kuti akamenyere ufulu wawo wachipembedzo womwe ndi wovomerezeka ndi malamulo a dzikoli.”

A Mboni za Yehova sachita zinthu zoopsa zimene zingasokoneze anthu. Misonkhano yawo imaphunzitsa anthu kuti azikonda Mulungu ndiponso anzawo. Mlungu uliwonse a Mboni a ku Taganrog amakambirana mfundo zofanana ndi zimene a Mboni anzawo amakambirana padziko lonse. Ngakhale kuti akuluakulu a boma ku Russia akhala akuwachitira zinthu zankhanza maulendo oposa 1,700, a Mboniwo sanabwezerepo.

A Mboni za Yehova akufuna kuti akuluakulu a boma ku Russia azindikire kuti chipembedzo cha Mboni za Yehova chimalimbikitsa mtendere ndipo asiye kuwaimba mlandu ku Taganrog ndiponso kumadera ena. Akuluakuluwo ayenera kupatsa a Mboni za Yehova ufulu wachipembedzo ngati mmene amachitira ndi azipembedzo zina zovomerezeka ndi boma.

Zimene Zinachitika pa Nthawi Yozenganso Mlanduwu b

  1. 22 January 2015

    Mlandu wa a Mboni 16 aja unayamba kuzengedwanso kukhoti la mumzinda wa Taganrog

  2. June 2015

    Woweruza anaimitsa kaye mlanduwu mpaka cha mu October

  3. 13 November 2015

    Woweruza anaimitsanso mlanduwo kuti aganizire chigamulo choyenera

  4. 30 November 2015

    Khoti la mumzinda wa Taganrog linagamula kuti a Mboni onse 16 ndi olakwa. Onse analipiritsidwa chindapusa ndipo 4 anapatsidwa chilango chokakhala mundende zaka zoposa 5. Kenako woweruza anauza anthuwo kuti sawatsekera kundende pa nthawiyo koma angatsekeredwe ngati atalakwitsa zinthu zina.

b Kuti mudziwe zimene zinachitika pa nthawi yozenga mlandu koyamba, onani nkhani yachingelezi yakuti, “Decision in Retrial Postponed for 16 of Jehovah’s Witnesses in Taganrog.”