Russia
Kucheza ndi Alongo 5: Akufotokoza Zimene Apolisi Anachita Mumzinda wa Ufa ku Russia
Ofufuza komanso gulu linalake la apolisi analowa n’kuchita chipikisheni m’nyumba za a Mboni ambiri. Azimayi a Mboni 5 awa akufotokoza mmene zimenezi zawakhudzira aliyense payekha.
A Mboni Enanso ku Russia Anamangidwa Apolisi Atathyola Nyumba Zawo
Akuluakulu a boma la Russia akhala akuchitira a Mboni zinthu zankhanza, kuwamanga komanso kuwaika m’ndende chifukwa chochita zinthu zokhudzana ndi chikhulupiriro chawo.
Wa Mboni Winanso ku Russia Akuimbidwa Mlandu Wochita Zinthu Zoopsa
A Arkadya Akopyan, ndi a Mboni za Yehova ndipo ali ndi zaka 70 komanso anapuma pa ntchito ya utelala. Bambowa ndi osalakwa, amamvera malamulo a boma ndipo cholinga chawo n’choti azipembedza Mulungu mwamtendere.
Khoti la ku Oryol Limvetsera Umboni Koyamba pa Mlandu wa a Dennis Christensen
A Dennis Christensen akhala akusungidwa m’ndende kuyambira mu May 2017. Iwo akhoza kupatsidwa chilango chokhala m’ndende kwa zaka 6 mpaka 10 chifukwa chongochita zinthu zogwirizana ndi zimene amakhulupirira.
Apolisi Ayamba Kuchitira Nkhanza a Mboni za Yehova ku Russia
Popeza kuti akuluakulu a boma la Russia anatseka mabungwe oimira Mboni za Yehova, tsopano ayamba kuukira munthu aliyense yemwe ndi wa Mboni komanso chilichonse chimene angachite chokhudza kulambira.
Akuluakulu a Boma ku Russia Akufuna Kulanda Malo ndi Nyumba za Bungwe la Mboni za Yehova la ku America
Mlandu wa apilo uyamba ku khoti la mu mzinda wa Saint Petersburg pa nkhani yofuna kulanda ofesi yakale ya Mboni za Yehova ku Russia.