Russia
Vidiyo Yosonyeza Apolisi ku Russia Akusokoneza Misonkhano ya Mboni za Yehova
Vidiyo yomwe bungwe lina lofalitsa nkhani ku Russia linatulutsa inasonyeza apolisi a Federal Security Service omwe anali ndi zida akusokoneza misonkhano imene a Mboni za Yehova ankapanga mumzinda wa Oryol ku Russia.
Vidiyo Yosonyeza Apolisi ku Russia Akusokoneza Misonkhano ya Mboni za Yehova
Pa 25 May 2017, apolisi a Federal Security Service (FSB) omwe anali ndi zida anasokoneza misonkhano imene a Mboni za Yehova ankachita mwamtendere mumzinda wa Oryol ku Russia.
A Mboni za Yehova Akuvutika Kwambiri Chifukwa cha Chigamulo cha Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia
Chigamulo cha khoti chachititsa kuti anthu ambiri azidana ndi a Mboni ndipo chapereka mphamvu kwa anthu komanso akuluakulu a boma kuti aziwachitira nkhanza.
Pulezidenti Putin Anapereka Mphoto kwa Makolo a Mboni za Yehova Chifuwa Cholera Bwino Ana Awo
Pa mwambo umene unachitikira kunyumba ya boma mumzinda wa Moscow, pulezidenti Vladimir Putin anapereka mphoto kwa a Valeriy ndi a Tatiana Novik, omwe ndi a Mboni za Yehova ndipo amakhala ku Karelia.
Khoti Lalikulu Kwambiri M’dziko la Russia Lagamula Kuti Likulu la Mboni za Yehova M’dzikolo Litsekedwe
A Mboni apanga apilo pa zimene khoti lagamula kuti likulu lawo m’dziko la Russia litsekedwe.
Mavuto Amene a Mboni Akhala Akukumana Nawo kwa Zaka 10 pa Nkhani Zamalamulo Anaunikidwa pa Tsiku la 5 Lozenga Mlandu ku Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia
Maloya oimira Unduna wa Zachilungamo sanathe kunena chifukwa chomveka chokhudza malamulo chochititsa kuti Likulu la Mboni za Yehova litsekedwe ku Russia.
A Mboni za Yehova Apereka Umboni Patsiku Lachitatu la Mlandu ku Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia
A Mboni 4 anafotokoza mfundo zofunika kwambiri zotsutsa zimene a Unduna wa Zachilungamo ananena zokhudza a Mboni m’dzikolo.
Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia Layamba Kuzenga Mlandu Waukulu Kwambiri Wokhudza Mboni za Yehova
Mlanduwu udzapitirira pa Lachinayi, 6 April , 2017.
Vasiliy Kalin: Zimene Woimira a Mboni Anayankhula Boma la Russia Litaopseza Kuti Liletsa Ntchito ya Mboni za Yehova M’dzikolo
Woimira Likulu la Mboni za Yehova m’dziko la Russia, a Vasiliy Kalin, akupempha akuluakulu a boma kuti asiye kuzunza a Mboni za Yehova popanda chifukwa.
A Mboni za Yehova Padziko Lonse Akulimbikitsidwa Kulemba Makalata Opempha Kuti Boma la Russia Lisaletse Ntchito Yawo M’dzikolo
Boma la Russia laopseza kuti liletsa ntchito ya Mboni za Yehova m’dzikolo. Choncho a Mboni za Yehova padziko lonse aganiza zolemba makalata opita ku boma la Russia ndiponso kwa akuluakulu a Khoti Lalikulu m’dzikolo. Pali malangizo omwe angathandize aliyense amene akufuna kulemba nawo makalatawa.