Russia
Khoti la Taganrog Linapereka Chilango kwa a Mboni Chifukwa Chochita Zachipembedzo
A Mboni onse 16 anapezeka kuti ndi olakwa pa mlandu wochita zinthu zoopsa zobweretsa chisokonezo. Chigamulochi chikhoza kuchititsa kuti a Mboni am’madera ambiri ku Russia aziimbidwa mlandu chifukwa chochita zachipembedzo.
Khoti la ku Taganrog Lagamula kuti a Mboni za Yehova 16 Ndi Olakwa Chifukwa Chochita Zachipembedzo
Chigamulochi chingachititse kuti a Mboni apitirize kuzunzidwa ndiponso kumangidwa chifukwa cha chipembedzo chawo ku Russia.
Zimene Mneneri wa Mboni za Yehova Ananena Zokhudza Mlandu wa ku Taganrog, M’dziko la Russia
Kuyambira mu 2011, a Mboni 16 akhala akuimbidwa mlandu chifukwa chochita zachipembedzo chawo. Kodi n’zoona kuti ali ndi mlandu wochita zinthu zoopsa zimene zingabweretse chisokonezo?
Akatswiri Ena Sanagwirizane ndi Zimene Dziko la Russia Lachita Poletsa JW.ORG
Pa 21 July 2015 dziko la Russia linaletsa webusaiti yovomerezeka ya Mboni za Yehova ya jw.org ndipo dzikoli ndi loyamba kuchita zimenezi.
Wa Mboni Wina wa ku Russia Anatola Ndalama Zokwana Mayuro 6,000 Ndipo Anazibweza kwa Mwini Wake
Mayi Svetlana Nemchinova, omwe ndi a Mboni za Yehova, anafufuza mwini wa ndalama zomwe zinatayidwa mwangozi pamalo ena.
Kodi Khoti la Rostov Ligamula Zotani pa Mlandu Umene a Mboni za Yehova Apanga Apilo?
Pa December 11, 2014, khoti la m’chigawo cha Rostov lidzamvetsera mlandu wa apilo wa a Mboni za Yehova 16 a ku Taganrog, m’dziko la Russia. Iwo akuimbidwa mlandu womwe akuti anachita zinthu zosokoneza maganizo a anthu.
Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia Lipitiriza Kuzenga Mlandu Wokhudza Kutsekedwa kwa Bungwe la Mboni la ku Samara
Pa November 12, 2014, Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia lakonza zoti lipitirize kuzenga mlandu wa apilo wokhudza kutsekedwa kwa bungwe lovomerezeka ndi boma la Russia la Mboni za Yehova la ku Samara.
A Mboni za Yehova a ku Samara Apanga Apilo Mlandu Wokhudza Kutsekedwa kwa Bungwe Lawo Lovomerezeka ndi Boma Kukhoti Lalikulu Kwambiri la ku Russia
Khoti Lalikulu Kwambiri la ku Russia liweruza mlandu umene a Mboni za Yehova a ku Samara apanga apilo. Mlanduwu ndi wokhudza kutsekedwa kwa bungwe lawo lovomerezeka ndi boma komanso woti bungweli limachita zinthu monyanyira komanso zosokoneza maganizo a anthu.
Khoti la ku Taganrog Lapeza a Mboni za Yehova Kuti ndi Olakwa Chifukwa Chochita Zinthu Zokhudzana ndi Chipembedzo Chawo
Ufulu wolambira wa a Mboni 160,000 ku Russia, uli pangozi chifukwa cha chigamulochi.
A Mboni za Yehova Akuimbidwa Mlandu ku Taganrog
Anthu akuphwanyiridwa ufulu wachipembedzo ku Russia. Mvetserani zimene ena mwa a Mboni 16 komanso maloya awo ananena.
Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Ladzudzulanso Boma la Russia Chifukwa Chophwanyira Anthu Ufulu Wachipembedzo
Chigamulo chachitatuchi chikusonyeza kuti Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya likuona kuti dziko la Russia likuphwanya ufulu wachibadwidwe wa a Mboni za Yehova, monga ufulu wolambira mwamtendere.