SEPTEMBER 2, 2019
RWANDA
A Mboni za Yehova Anapanga Msonkhano Wachigawo Woyamba wa Chinenero Chamanja cha ku Rwanda
Abale athu ku Kigali m’dziko la Rwanda anapanga msonkhano wachigawo woyamba wa Chinenero Chamanja cha ku Rwanda kuyambira pa 16 mpaka 18 August, 2019. Pamsonkhanowu panali anthu 620 ndipo anthu 8 a vuto losamva anabatizidwa.
Akuluakulu awiri a mabungwe a anthu olumala anabwera kumsonkhanowu Lamlungu. Mayina awo ndi a Jean Damascène Bizimana omwe ndi membala wa gulu la madailekitala a bungwe la Rwanda National Union of the Deaf, komanso a Emmanuel Ndayisaba omwe ndi mlembi wamkulu wa bungwe la National Council of Persons with Disabilities. Kuwonjezera pamenepo, a nyuzipepala ya Ukwezi anapezeka pamsonkhanowu Lamlungu ndipo analemba lipoti labwino pa intaneti.
A Bizimana anati: “Msonkhanowu unali wabwino kwabasi! Zinali zosangalatsa kwambiri kuona anthu a vuto losamva ochokera m’madera osiyanasiyana a m’dziko muno ali pamodzi. Tikuyamikira kwambiri a Mboni za Yehova chifukwa chothandiza kuti anthu a vuto losamva azitha kulumikizana. Akuluakulu a boma abwere kuti adzaone mmene msonkhanowu wathandizira anthu kukhala ogwirizana ndipo nawonso atengerepo chitsanzo.”
M’zaka ziwiri zapitazi, m’gawo la Chinenero Chamanja cha ku Rwanda munachitika zinthu zinanso ziwiri zosaiwalika. Mwachitsanzo, mu September 2017, ofesi ya nthambi ya Rwanda inachititsa Sukulu ya Utumiki Waupainiya yoyamba m’Chinenero Chamanja cha ku Rwanda. Patangotha chaka chimodzi, mu September 2018, ntchito yomasulira mabuku ndi zinthu zina m’Chinenero Chamanja cha ku Rwanda inayamba pa ofesi ya nthambiyi.
M’bale Jean d’Amour Habiyaremye yemwe anaimira ofesi ya nthambi pamsonkhanowu, anati: “Tikusangalala kwambiri kuona mmene zinthu zikupitira patsogolo m’gawo la Chinenero Chamanja cha ku Rwanda, zomwe zikuphatikizapo msonkhano wachigawo waposachedwapa umenewu. Zimene mutu wa msonkhanowu ukunena zoti ‘Chikondi Sichitha’, zikukwaniritsidwa tikaona mmene a Mboni za Yehova amasonyezera chikondi kwa anthu onse, kuphatikizapo anthu a vuto losamva.”
Kupita patsogolo kwa zinthu m’gawo la chinenero cha manja ndi umboni woonekeratu wosonyeza kuti Yehova akupitiriza kutidalitsa.—Salimo 67:1.