Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Nyumba ya m’bale wina yomwe inaonongeka kwambiri ndi mvula yamphamvu

NOVEMBER 19, 2019
RWANDA

Mvula Yamphamvu Kwambiri Yaononga ku Rwanda

Mvula Yamphamvu Kwambiri Yaononga ku Rwanda

Pa 26 ndi 29 October, 2019, mvula yamphamvu inagwa m’madera akuluakulu kumpoto kwa dziko la Rwanda. Mabanja ambiri a Mboni za Yehova anakhudzidwa ndi mvulayi. Tili ndi chisoni chachikulu chifukwa choti mtsikana wazaka 13 wa m’banja lina la Mboni anafa atakokoloka ndi madzi osefukira m’boma la Musanze m’chigawo chakumpoto kwa dzikoli.

M’chigawo chakumadzulo m’boma la Ngororero, nyumba ya banja lina la Mboni inaonongeka ndipo mbewu za mabanja 9 zinaonongekanso. Ofesi ya nthambi ya Rwanda ikuyendetsa ntchito yothandiza anthu m’chigawochi, kuphatikizapo kupereka ndalama komanso kuwalimbikitsa pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo.

Tikupemphera kuti Yehova apitirize kutonthoza mitima ya abale athu omwe akuvutika chifukwa cha ngoziyi.—2 Atesalonika 2:16, 17.