JUNE 9, 2016
RWANDA
Boma la Rwanda Lathetsa Tsankho Limene Limachitika M’masukulu Chifukwa cha Kusiyana kwa Zipembedzo
Boma la Rwanda linachitapo kanthu ndi cholinga chofuna kuthetsa tsankho limene limachitika m’masukulu chifukwa cha kusiyana kwa zipembedzo. Bomali linapereka lamulo loti zimene ana a sukulu amakhulupirira ziyenera kulemekezedwa. Imeneyitu ndi nkhani yosangalatsa kwambiri kwa ana a sukulu amene safuna kuchita nawo zinthu zina zimene zimachitika pa sukulu chifukwa cha zimene amakhulupirira.
Ku Rwanda, m’sukulu zambiri boma ndi limene limalipira mbali ina ya ndalama zimene ana a sukulu amalipira monga fizi koma sukuluzi zimayendetsedwa ndi magulu a zipembedzo. Chifukwa chakuti wina aliyense akhoza kumakaphunzirako, ana a m’sukuluzi akhoza kukhala a m’zipembedzo zosiyanasiyana. Komabe, akuluakulu a sukulu zina amalimbikitsa kwambiri zoti ana azichita zinthu zogwirizana ndi chipembedzo chomwe chikuyendetsa sukuluyo, azikonda kwambiri dziko lawo komanso kupereka msonkho wa ku tchalitchi. Ana amene amakana kuchita zimenezi chifukwa cha zimene amakhulupirira, amawapatsa chilango. Nduna ya boma imene imayang’anira maphunziro a ku pulayimale komanso ku sekondale inafotokoza maganizo amene akuluakulu ambiri oyendetsa sukulu zimenezi ali nawo ndipo inati: “Ana a sukulu ayenera kupembedza Mulungu m’njira yokhayo imene ikugwirizana ndi zimene ifeyo timakhulupirira.”
Zimene Boma Linalamula Zalimbikitsa Ufulu wa Ana a Sukulu Wochita Zinthu Mogwirizana ndi Zimene Amakhulupirira
Akuluakulu a boma analowererapo ndi cholinga chofuna kuthetsa vutoli ndipo anapereka lamulo lokhala ndi mfundo zatsopano zimene cholinga chake ndi kuthetsa tsankho limene limachitika m’masukulu chifukwa cha nkhani za chipembedzo. Gawo 12 la lamulo nambala 290/03 lomwe linafalitsidwa pa 14 December, 2015 mu buku lotchedwa Official Gazette, linanena kuti sukulu iliyonse iyenera kulemekeza ufulu wopembedza umene ana a sukulu ali nawo. Linanenanso kuti ana a sukuluwo ayenera kuloledwa kupemphera mogwirizana ndi zimene amakhulupirira ngati chipembedzo kapena tchalitchi chawocho ndi chovomerezeka mwalamulo komanso ngati kuchita zimenezo sikukusokoneza maphunziro pasukulupo.
Lamulo Nambala 290/03, Gawo 12, limanena kuti Sukulu iliyonse iyenera kulemekeza ufulu wopembedza umene ana a sukulu ali nawo.
Zimene boma linachitazi zikugwirizana kwambiri ndi zimene khoti la ku Karongi linagamula pa mlandu wina wa ana a sukulu a Mboni omwe anachotsedwa sukulu mu May 2014. Akuluakulu a pasukulupo sanagwirizane ndi zimene anawo anachita pokana kuchita nawo msonkhano wachipembedzo umene unakonzedwa ndi sukuluyo. Khoti la ku Karongi linagamula kuti anawo anali osalakwa ndipo analoledwa kupitiriza maphunziro awo.
M’chigawo china chotchedwa Ngororero, mphunzitsi wamkulu wa pasukulu ina anakana kupereka ma sukulu lipoti kwa ana 30 amene anakana kupereka msonkho wa ku tchalitchi. Msonkhowu sukugwirizana ndi sukulu fizi. Makolo a anawa atakadandaula kwa mkulu woyang’anira maphunziro m’chigawochi, mphunzitsi wamkuluyo anasintha maganizo ndipo anapatsa anawo ma sukulu lipoti awo pamene ankatsekera.
Ana a Sukulu a Mboni Tsopano ali pa Mtendere
Chantal Uwimbabazi yemwe amakhala m’chigawo cha Ngororero ndipo ndi wa Mboni, anachotsedwa sukulu chifukwa chokana kuchita nawo mwambo wa Misa wa tchalitchi cha Katolika umene sukuluyo inkachita. Iye ananyozedwa kwambiri ndi ana asukulu a m’kalasi mwake komanso anthu ena ndipo sanathenso kuphunzira kwa chaka chathunthu. Kenako anayamba kuphunzira pa sukulu ina yomwe inali yodula kwambiri komanso inali kutali ndi kwawo. Izi zinali zovuta kwambiri chifukwa bambo ake anali atamwalira ndipo mayi ake ankavutika kuti apeze ndalama. Chantal anasangalala kwambiri atamva za malamulo atsopano amene boma linakhazikitsa. Iye ananena kuti: “Ndikuganiza kuti ana amene ali m’sukulu zoyendetsedwa ndi gulu la chipembedzo, amene akukumana ndi zimene ndinakumana nazo ine, akhala ndi mwayi wophunzira popanda kuwaphwanyira ufulu wawo.”
Lamulo latsopanoli ndi logwirizana ndi malamulo oyendetsera dziko la Rwanda, omwe amapereka ufulu wopembedza komanso ufulu wa maphunziro. Ana a sukulu omwe ndi a Mboni za Yehova limodzi ndi makolo awo, akuyembekezera mwachidwi kutha kwa tsankho limene limachitika chifukwa cha kusiyana kwa zipembedzo. Iwo akuyamikira kwambiri zimene boma lachita poteteza ufulu wopembedza wa ana asukulu.