Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Banja la ku Sierra Leone lanyamula Mabaibulo awo atsopano a Malemba Achigiriki mu Chikiliyo, pambuyo poonera nkhani ya kutulutsidwa kwa Baibuloli pa TV ya boma

MAY 4, 2020
SIERRA LEONE

Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu Layamba Kupezeka mu Chikiliyo

Baibuloli Linatulutsidwa ku Sierra Leone Kudzera pa Wailesi ya Boma ndi pa TV

Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu Layamba Kupezeka mu Chikiliyo

Pa 26 April 2020, ofalitsa oposa 2,000 omwe amalankhula Chikiliyo ku Sierra Leone anasangalala ndi kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu.

Zinali zosatheka kuti abale athu asonkhane pamodzi pa nthawi yotulutsa Baibuloli chifukwa boma linaika malamulo oletsa kusonkhana popewa kufalikira kwa mliri wa kolonavairasi. Kuwonjezera pamenepo, abalewo sakanathanso kuonera pulogalamu yapaderayi pa nthawi yomwe inkachitika, chifukwa ofalitsa ambiri ku Sierra Leone, makamaka amene amakhala m’mizinda ing’onoing’ono alibe zipangizo zamakono.

M’bale Alfred Gunn wa m’Komiti ya Nthambi ya Liberia, akutulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu m’Chikiliyo

Pasanapite nthawi, Komiti ya Nthambi ya ku Liberia yomwe imayang’anira mmene ntchito yathu ikuyendera ku Sierra Leone, inapempha Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa ya Bungwe Lolamulira kuti iwalole kujambula chidule cha pulogalamu yotulutsa Baibuloyo. Ndiyeno ofalitsa anauzidwa kuti amvetsere pawailesi kapena aonere pa TV pulogalamu yapaderayo. Koma ofalitsawo sanauzidwe zoti patulutsidwa Baibulo.

Patangotsala masiku ochepa kuti pulogalamuyo ichitike, ofalitsa analandira maenvelopu omatidwa bwino muli Mabaibulo mkati mwake. Maenvelopuwo anatumizidwanso ndi malangizo oti ofalitsawo asawatsekule mpaka pulogalamu yapaderayo itachitika.

Baibuloli litatulutsidwa, Mlongo Megan Diaz wa ku Sierra Leone, yemwe ankalifunitsitsa kwambiri, ananena kuti: “Amene ndimaphunzira naye Baibulo anandiimbira foni n’kundiuza kuti anapeza nthawi yomvetsera nkhani yomwe inakambidwa komanso kuti akusangalala chifukwa Yehova wathandiza kuti Baibuloli limasuliridwe. Tigwiritsa ntchito Baibulo limeneli pophunzira mawa.”

Tounkara yemwe amalankhula Chikiliyo ndipo amaphunzira Baibulo ananena kuti: “Kutulutsidwa kwa Baibulo la Malemba Achigiriki mu Chikiliyo ndi umboni wosonyeza kuti Yehova akufuna kuti uthenga wake ufikire aliyense komanso kuti anthu azitha kuumvetsa bwino n’cholinga choti aziphunzitsanso ana awo. Ndasangalala kwambiri ndi kutulutsidwa kwa Baibulo latsopanoli m’chilankhulo chathu.”

Chikiliyo ndi chilankhulo chotengedwa kuchingelezi ndipo anthu ambiri ku Sierra Leone amalankhula chinenerochi. Panatenga zaka ziwiri ndi hafu kuti omasulira 4, amasulire Baibulo la Malemba Achigiriki mu Chikiliyo. Pofika Lolemba pa 27 April, linayamba kupezeka pa zipangizo zamakono kuti anthu azitha kupanga dawunilodi.

Tonsefe limodzi ndi abale komanso alongo athu ku Sierra Leone, tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa cha kutulutsidwa kwa Baibulo la Malemba Achigiriki mu Chikiliyo. Imeneyinso ndi ‘mphatso yabwino ndi yangwiro’ yochokera kwa Atate wathu wakumwamba, Yehova.—Yakobo 1:17