Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

AUGUST 14, 2019
SLOVAKIA

Msonkhano Wachigawo Woyamba M’chinenero cha Chiromane (Kum’mawa kwa Slovakia)

Msonkhano Wachigawo Woyamba M’chinenero cha Chiromane (Kum’mawa kwa Slovakia)

Mmodzi mwa anthu 19 akubatizidwa

Kuyambira pa 20 mpaka 21 July, 2019, abale athu anachititsa msonkhano wachigawo woyamba wa chinenero cha Chiromane ku Slovakia, womwe unachitikira pa Winter Stadium m’tawuni ya Michalovce. Msonkhanowu unali wamasiku awiri ndipo chiwerengero cha osonkhana chinali 1,276. Anthu 19 anabatizidwa.

Ena mwa abale ndi alongo omwe anali pamsonkhanowu anali alendo ochokera ku Belgium, Czech Republic, Great Britain, ndi Ukraine. Anthu pamsonkhanowu anasangalala kwambiri kuonera vidiyo yakuti Nkhani ya Yosiya Imatiphunzitsa Kukonda Yehova Komanso Kudana ndi Zoipa, m’chinenero chawo chobadwira.

Msonkhano wachigawowu wachitika patangotha zaka 5 kuchokera pamene mpingo woyamba wa Chiromane unakhazikitsidwa ku Slovakia mu November 2014. Panopa, m’gawo la nthambi ya Czech-Slovak muli mipingo 9 ya Chiromane, magulu 10, komanso timagulu 14.

A Peter Tirpak, omwe ndi mkulu wa Winter Stadium, anati: “Sitinavutike kuchita nanu zinthu a Mboni za Yehova. Mwakhala mukuchita zomwe munanena kuti muchita. Tidzasangalala mukadzabweranso.”

A Peter Varga, omwe anali woyang’anira pulogalamu pamsonkhanowu, anati: “Sindinaonepo msonkhano ngati umenewu. Umenewu unali msonkhano wofunika kwambiri kwa abale ndi alongo athu oyankhula Chiromane, ndipo sadzauiwala. Nyimbo yomaliza itatha, iwo anayamba kuhagana ngakhale kuti anali asanakumanepo m’mbuyomu. Ambiri ankagwetsa misozi.”

Tikusangalala limodzi ndi ofalitsa 1,010 omwe amayankhula Chiromane ku Slovakia. Misonkhano yachigawo imasonyeza chikondi chenicheni chomwe chili pakati pa anthu a Yehova.—Yohane 13:34, 35.