AUGUST 20, 2019
SOUTH AFRICA
A Mboni za Yehova Atulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chikwanyama
Pa 16 August, 2019, a Mboni za Yehova anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chikwanyama pa msonkhano wachigawo womwe unachitikira m’tawuni ya Ondangwa ku Namibia. M’bale Franco Dagostini wa m’Komiti ya Nthambi ya South Africa ndi amene anatulutsa Baibuloli pa tsiku loyamba la msonkhanowu womwe unachitikira pa Ondangwa Trade Fair Hall.
Mmodzi mwa anthu omwe anamasulira nawo Baibuloli anati: “Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu lithandiza anthu kuwerenga ndiponso kumvetsa uthenga wa m’Baibulo mosavuta. Abale ndi alongo athu asangalala kuona dzina la Yehova m’malo amene liyenera kupezeka.”
M’gawo la nthambi ya South Africa muli ofalitsa pafupifupi 490 oyankhula Chikwanyama. Ofalitsawa amalalikira kwa anthu pafupifupi 1.4 miliyoni oyankhula Chikwanyama omwe ambiri ndi a ku Angola ndi Namibia.
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika tsopano lamasuliridwa lathunthu kapena mbali zake zina m’zinenero 184, kuphatikizapo m’zinenero 25 zomwe zakonzanso Mabaibulo awo mogwirizana ndi Baibulo lomwe linatulutsidwa mu 2013. Ndife osangalala kwambiri kudziwa kuti abale ndi alongo athu agwiritsa ntchito Baibuloli polalikira kwa anthu ambiri oyankhula Chikwanyama.—Machitidwe 2:37.