Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

SEPTEMBER 13, 2019
SOUTH AFRICA

Baibulo la Dziko Latsopano Latulutsidwa M’ziyankhulo Zitatu Pamsonkhano Wamayiko ku South Africa

Baibulo la Dziko Latsopano Latulutsidwa M’ziyankhulo Zitatu Pamsonkhano Wamayiko ku South Africa

Pamsonkhano wamayiko womwe unachitikira mumzinda wa Johannesburg ku South Africa pa 6 September, 2019, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika linatulutsidwa m’zinenero za Chivenda, Chiafirikana, ndi Chikhosa, ndipo zinenerozi zimalankhulidwa ndi anthu oposa 16 miliyoni. M’bale Anthony Morris wa m’Bungwe Lolamulira analengeza za kutulutsidwa kwa Mabaibulowa kwa anthu 36,865 omwe anasonkhana pa FNB Stadium. Anthu enanso 51,229 anamvetsera msonkhanowu m’malo ena 8, ndipo malowa akuphatikizapo ku Lesotho, Namibia, ndi ku Saint Helena.

Poyankhulapo pa zinthu zapadera zomwe zili m’Mabaibulowa, mosangalala womasulira wina anati: “Ndife osangalala kwambiri kuti tiwerenga Baibulo lonse m’chinenero chomwe chimatifika pamtima.” Womasulira winanso anati: “Chofunika kwambiri n’choti, [Baibulo lomwe latulutsidwa kumeneli] litithandiza kuyandikira kwambiri Yehova chifukwa dzina la Mulungu lagwiritsidwa ntchito mobwerezabwereza m’Baibuloli.”

Mabaibulowa athandizanso kwambiri abale athu akamalalikira. Mmodzi mwa anthu omwe anamasulira nawo Baibulo la Chikhosa anati: “Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso lithandiza muutumiki. Anthu azimva mosavuta zimene Baibulo limaphunzitsa popanda kuwafotokozera zomwe mawu ena alionse akutanthauza.” Womasulira wa Chiafirikana anaonjezera kuti: “Tsopano ukhoza kungowerenga lemba, mfundo yapalembalo n’kumveka popanda kufotokoza.”

Tikusangalala kuti abale athu ali ndi Mabaibulo osavuta kuwerenga omwe awathandize kuyandikira kwambiri Mulungu wathu.—Yakobo 4:8.