Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JUNE 5, 2019
SOUTH AFRICA

Mvula Yamphamvu Komanso Madzi Osefukira Zachititsa Mavuto ku South Africa

Mvula Yamphamvu Komanso Madzi Osefukira Zachititsa Mavuto ku South Africa

Chakumapeto kwa mwezi wa April 2019, mvula yamphamvu inagwa m’dera lomwe lili m’mphepete mwa nyanja chakum’mawa kwa dziko la South Africa. Mvulayi inagwa mowirikiza kwambiri zomwe zinachititsa kuti madzi asefukire komanso kuti matope akokoloke m’madera ambiri a mumzinda wa Durban ndiponso m’madera ena ozungulira mzindawu, womwe uli m’chigawo cha KwaZulu-Natal. Malipoti ochokera kwa ofalitsa nkhani akusonyeza kuti anthu osachepera 70 afa.

Ofesi ya nthambi ya ku South Africa yanena kuti palibe m’bale kapena mlongo amene wavulala kapena kufa. Komabe, nyumba za mabanja osachepera 19 zinaonongeka chifukwa cha matope okokoloka kapena madzi osefukira. Nyumba za Ufumu zosachepera zitatu zinaonongeka ndi madzi osefukira.

Mogwirizana ndi malangizo ochokera ku Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi, abale ongodzipereka a m’Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga akufufuza kuti aone mmene nyumba iliyonse yawonongekera. Ngati miyoyo ya abale ili pachiopsezo chifukwa cha kumene akukhala, iwo akumapatsidwa malo ena okhala.

Tikukhulupirira kuti Yehova apitiriza kuthandiza abale ndi alongo athu ku South Africa pa nthawi yovutayi.—Salimo 34:19.