22 FEBRUARY 2023
SOUTH AFRICA
Nthambi ya ku South Africa Yatsegula Ofesi Yatsopano ya Omasulira Mabuku a Chilankhulo cha Chivenda
Pa 7 December 2022, ofesi ya omasulira mabuku a Chivenda inatsegulidwa ku Makhado m’dziko la South Africa. Pa ofesiyi pali omasulira 10 omwe amatumikira kwa masiku onse pa mlungu ndipo 8 amatumikira kwa masiku ochepa pa mlungu.
Ku South Africa kuli anthu pafupifupi 1.2 miliyoni olankhula Chivenda pomwe ku Zimbabwe alipo 100,000. Panopa m’mayiko awiri amenewa muli mipingo 28 ya chilankhulo cha Chivenda yomwe ili ndi ofalitsa pafupifupi 800.
Pamalo pomwe pali ofesiyi, panali kale nyumba imene inakonzedwanso kuti ikhale nyumba zokwanira 4 zogonamo. Anamanganso nyumba yatsopano kuti azigwiriramo ntchito yomasulira. Panagulidwanso nyumba zina zitatu chapafupi kuti ena azikhalamo.
Ofesiyi inamangidwa m’njira yoti izigwirizana ndi nyengo ya m’deralo. Mwachitsanzo, M’bale Jody Palvie, yemwe amagwira ntchito ngati woyang’anira pulojekiti mu Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga, anati: “Kunoko kumatentha kwambiri, choncho tinasiya mitengo ikuluikulu kuti izibweretsa mthunzi komanso tinagwiritsa ntchito matailosi ndi konkire yopolisha kuti m’nyumbazi muzikhala mozizira.”
Maofesi atsopanowa akuthandiza kuti abale ndi alongo omasulira azichita zinthu mosavuta ndi anthu olankhula Chivenda. Womasulira wina ananena kuti: “Panopa tsiku lililonse tikumatha kulankhula ndi anthu omwe Chivenda ndi chilankhulo chawo wobadwira. Zimenezi zikumathandiza kuti tiwonjezere luso lomasulira, chifukwa tikumatha kugwiritsa ntchito mawu omwe anthu amalankhula tsiku ndi tsiku.” Womasulira wina anati: “Panopa tikukhala pafupi ndi abale ndi alongo olankhula Chivenda omwe angamatithandize pojambula mavidiyo ndi zinthu zongomvetsera.”
Tikudziwa kuti Yehova apitiriza kudalitsa zimene abale ndi alongo athuwa akuchita poyesetsa ‘kulankhula zotamanda Yehova’ kwa anthu olankhula Chivenda.—Salimo 145:21.