SEPTEMBER 16, 2019
SOUTH AFRICA
Zokhudza Msonkhano Wamayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Johannesburg, South Africa
Masiku: 6 mpaka 8 September, 2019
Malo: FNB Stadium ku Johannesburg, South Africa
Zinenero: Chingelezi, Chisutu, Chizulu
Chiwerengero cha Osonkhana: 58,149
Chiwerengero cha Obatizidwa: 476
Chiwerengero cha Alendo Ochokera Kumayiko Ena: 6,000
Nthambi Zoitanidwa: Bolivia, Britain, Central Europe, Congo (Kinshasa), Finland, Hong Kong, Hungary, Israel, Japan, Kenya, Korea, Liberia, Madagascar, Malawi, Paraguay, Peru, Uganda, United States, Zambia, ndi Zimbabwe
Zina Zomwe Zinachitika: Akuluakulu a malo osungirako zinyama otchedwa Lion and Safari Park, omwe ndi amodzi mwa malo omwe alendo ochokera kumayiko ena anapita, ananena kuti sanaonepo anthu a zikhalidwe ndi zilankhulo zosiyanasiyana akutsika m’basi imodzi popanda kukangana kapena kudandaula. Akuluakuluwa anasangalala kwambiri ndi mmene alendowa ankachitira potsatira malangizo komanso kumvera anthu ogwira ntchito kumalowa. Iwo anati: “Zinali zosangalatsa kukhala ndi alendowa.”
Abale ndi alongo akulandira alendo ochokera kumayiko ena
Alongo awiri a ku South Africa ndi awiri ochokera kumayiko ena ali muutumiki ndipo akugawira timapepala toitanira anthu kumsonkhano
Abale ndi alongo akujambulitsa atavala zovala zakwawo
Abale ndi alongo akumwetulira komanso kuombera m’manja msonkhano uli mkati
Mmodzi mwa anthu 476 akubatizidwa
M’bale Anthony Morris wa m’Bungwe Lolamulira akupereka moni kwa abale ndi alongo pa nthawi yopuma
Pa tsiku lomaliza la msonkhanowu, alendo omwe ali muutumiki wa nthawi zonse wapadera anauzidwa kuti apite m’bwalo la malo a msonkhano kuti anthu awaone
Alongo atatu akujambulitsa msonkhanowu utatha
Gulu la oimba lomwe lavala zovala zokongola za ku Africa likuimba pa zochitika zosangalatsa zomwe zinachitika madzulo