MAY 26, 2020
SOUTH KOREA
Akuluakulu Ena ku South Korea Anayamikira a Mboni za Yehova Chifukwa Chosankha Kuchita Misonkhano Kudzera pa Intaneti
Akuluakulu omwe amayang’anira malo ochitira misonkhano yosiyanasiyana ku South Korea ayamikira gulu lathu chifukwa chokonza zoti msonkhano wathu wa 2020 uchitikire kudzera pa intaneti m’malo mosonkhana m’masitediyamu akuluakulu. Iwo anatiyamikira chifukwa chochita zimenezi zomwe zathandiza kuti anthu ambiri atetezeke kwinaku tikupitirizabe kulambira kwathu. Ndalama zonse zimene tinaperekeratu pokonzekera kuchita msonkhano kumalo osiyanasiyana atibwezera.
Mkulu wina yemwe amagwira ntchito kumalo ena ku Seoul anati: “Sitikudabwa kuti a Mboni za Yehova asankha kuchita zimenezi. Timawakonda kwambiri. Ndikukayikira ngati palinso chipembedzo china chimene chimachita zinthu zothandiza anthu a m’dera lawo ngati mmene a Mboni amachitira.” Iye anapitiriza kunena kuti: “A Mboni amachita zinthu zoganizira anthu ena. Tikudandaula kuti chaka chino satha kuchitira msonkhano wawo pamalo ano. Tikuyembekezera kuti adzagwiritsa ntchito malo athuwa m’tsogolo muno.”
Munthu wina ku Suwon anati: “Ndimathokoza kwambiri a Mboni za Yehova chifukwa choti akhala akugwiritsa ntchito malo ano kwa zaka 35 zapitazi ndipo akhala akuwasamalira bwino kwambiri ngati kuti ndi awo. Komano panopa ndikuwayamikira kwambiri chifukwa chotsatira malangizo a boma okhudza kupewa kufala kwa mliri wa COVID-19. Zandichititsa chidwi kwambiri kuona kuti amaganizira anthu ena. Ndikufunitsitsa kudzaonananso ndi a Mboni za Yehova chaka chamawa.”
Munthu winanso yemwe amagwira ntchito pabwalo la ndege lomwe lili pafupi ndi malo a msonkhano anati: “M’chaka cha 2018 ndi 2019, ndinaona mmene [a Mboni za Yehova] amachitira zinthu mwadongosolo komanso mmene ankatiyankhira mafunso athu. Iwo anasankha kuti asachitire msonkhano wawo chaka chino pamalowa chifukwa choganizira anthu ena ndipo ndikuona kuti achita bwino kwambiri.” Anapitirizanso kuti: “Tikuona kuti zinthu zikanakhala bwino kwambiri anthu onse akanamachita zinthu ngati a Mboniwa.”
Anthu a Yehovafe timayamikira kwambiri kuti timaphunzitsidwa mmene tingamasonyezere anzathu chikondi ndipo chikondi chimenechi chikuonekera kwambiri m’masiku ovuta ano.—Mateyu 22:39..