Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JANUARY 17, 2020
SOUTH KOREA

Chinthu Chapadera Chomwe Boma la South Korea Lachitira Okana Kulowa Usilikali

Chinthu Chapadera Chomwe Boma la South Korea Lachitira Okana Kulowa Usilikali

Pa 31 December, 2019, boma la South Korea linalengeza kuti lakhululukira mwapadera anthu 1,879 omwe anatulutsidwa m’ndende posachedwapa. Anthuwa anamangidwa atakana kulowa usilikali chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Ngakhale kuti abalewa akhalabe ndi mbiri yoti anapalamulapo mlandu, boma liwalola kuyambiranso kuchita zinthu zomwe linawaletsa. Zimene boma lachitazi zikugwirizana ndi zigamulo zomwe zinaperekedwa ndi Khoti Lalikulu Loona za Malamulo komanso Khoti Lalikulu Kwambiri m’chaka cha 2018. Zigamulozi zinanena kuti munthu akakana kulowa usilikali chifukwa cha chikhulupiriro chake sikuti wapalamula mlandu koma ndi ufulu wake.

Ku Korea, anthu akamaliza kugwira ukaidi wawo kundende, boma limawaletsa kuchita zinthu zina kwa zaka 5. Popeza kuti anthu omwe akana kulowa usilikali amakhala ndi mbiri yoti anapalamula mlandu, boma linaletsa abale athuwa kuchita zinthu zina kwa zaka zimenezi. Chifukwa cha zimenezi, abalewa sanaloledwe kulemba mayeso a boma kuti akhale ndi ziphaso zovomerezeka kapena kufunsira ntchito zina.

M’bale Hong Dae-il yemwe amayang’anira Dipatimenti Yoona Zofalitsa Nkhani ku South Korea, anati: “Tikuthokoza kwambiri boma chifukwa chopereka ufulu umenewu kwa nzika zake. Chigamulochi chithandiza kuti boma lifike povomerezeratu kuti si mlandu kukana kulowa usilikali chifukwa cha zimene munthu amakhulupirira.”

Pamene tikuyembekezera zinthu zinanso zabwino zimene boma lingagamule m’tsogolo, tikupereka ulemerero ndi ulemu kwa Yehova yemwe ndi Wopereka Malamulo wamkulu.—Chivumbulutso 4:11.