Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Moto wolusa unatentha malo aakulu kwambiri m’zigawo ziwiri za ku South Korea ndipo zinthu zambiri zinawonongeka

15 MARCH, 2022
SOUTH KOREA

Moto Wolusa Unawononga M’zigawo ziwiri za ku South Korea

Moto Wolusa Unawononga M’zigawo ziwiri za ku South Korea

Kuyambira pa 4 March 2022, moto wolusa unawononga malo aakulu pafupifupi maekala 23,993 m’nkhalango ina. Ndipo zimenezi zinachititsa kuti anthu ambiri athawe m’nyumba zawo. Anthu ena akuti ngoziyi ikhoza kukhala yoopsa kwambiri kuposa ngozi iliyonse imene inachitikapo ku South Korea.

Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu

  • Ofalitsa 44 anachoka m’nyumba zawo

  • Nyumba imodzi inawonongekeratu

Ntchito Yopereka Chithandizo

  • Ofalitsa amene anakhudzidwa, anasungidwa kwa kanthawi ndi achibale awo komanso ofalitsa ena kumadera amene kunali bwino

  • Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi inakhazikitsidwa kuti ikapereke chithandizo

  • Amene akugwira ntchito yopereka chithandizoyi akutsatira njira zodzitetezera ku covid19

Sitikukayikira kuti Yehova adalitsa khama la abale ndi alongo amene akuyesetsa kuthandiza anzawo panthawi yovutayi.—Miyambo 17:17.