Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Abale atatu mwa abale 5 a ku Korea omwe khoti la m’boma la Jeonju linagamula posachedwapa kuti ndi osalakwa.

JANUARY 23, 2019
SOUTH KOREA

“Ndi Osalakwa”

Kwa Nthawi Yoyamba, Khoti ku South Korea Lagamula Kuti Okana Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira Alibe Mlandu

“Ndi Osalakwa”

Kwa nthawi yoyamba m’dziko la South Korea, maloya oimira boma anapempha khoti la apilo kupereka chigamulo choti abale athu 5 omwe ankaimbidwa milandu chifukwa chokana kulowa usilikali ndi osalakwa. Choncho khotilo linamasula abalewa ndipo linathetseratu milandu yawo. Chigamulochi chinasinthiratu chigamulo cha makhoti aang’ono omwe anagamula kuti abale athuwa ndi olakwa chifukwa chozemba usilikali.

Chigamulochi chinapangidwa pa 14 December, 2018, ndipo chithandiza oweruza a m’makhoti osiyanasiyana a ku Korea kuti aweruze mokomera abale athu oposa 900 omwenso akuyembekezera kuzengedwa milandu yokana usilikali. Abale omwe milandu yawo yathetsedwawa akuyembekezera kukhazikitsidwa kwa dongosolo loti anthu omwe akana usilikali azipatsidwa ntchito zina.

Khoti la apilo linapanga chigamulochi pogwiritsa ntchito zigamulo zosaiwalika za mu 2018 zomwe zinapangidwa ndi Khoti Loona Zamalamulo Oyendetsera Dziko komanso Khoti Lalikulu Kwambiri ku Korea. Zigamulozi zinathetsa lamulo lomwe lakhala likugwira ntchito kwa zaka 65 m’dziko la Korea. Lamulolo linkanena kuti aliyense yemwe wakana usilikali ayenera kupita kundende ngakhale atakana pazifukwa zomveka zokhudza chipembedzo.

Mabungwe oona za maufulu a anthu anayamikira kwambiri zigamulo zomwe makhoti awiriwa anapanga chifukwa analemekeza ufulu womwe anthu ali nawo wokana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Bungwe Loona za Ufulu wa Anthu ku Korea linati: “Chigamulo chomwe chinapangidwa ndi oweruza onse a Khoti Lalikulu Kwambiri chinathetsa mchitidwe wopereka chilango kwa okana usilikali, womwe unayamba m’ma 1950 ndipo unakhudza anthu pafupifupi 20,000 . . . Tikupereka ulemu waukulu kwa anthu omwe anakana usilikali komanso mabanja awo chifukwa chopirira mavuto omwe anakumana nawo.”

Panopa, anthu omwe akukana usilikali chifukwa cha chikhulupiriro chawo akumauzidwa kuti apereke umboni wotsimikizira kuti akukana chifukwa choti zomwe amakhulupirirazo ndi “zenizeni ndipo sizingasinthe.” Oweruza milandu alangizidwa kuti azipeza umboni wosonyeza kuti zimene wokana usilikaliyo amakhulupirira n’zoonadi. Khoti Lalikulu Kwambiri linanena kuti: “Zonse zimene munthuyo amachita pa moyo wake . . . ziyenera kugwirizana ndi zomwe amakhulupirira kwambirizo.” Abale athuwa akamayankha mafunso amene oweruza milandu akuwafunsa, azipezerapo mwayi wofotokoza momveka bwino chifukwa chimene anasankhira kukana kumenya nkhondo komanso kugwira ntchito ya usilikali.—1 Petulo 3:15.

Kwa zaka zoposa 60, a Mboni za Yehova ku Korea akhala akuikidwa m’ndende chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zomwe amakhulupirira. Umenewu ndi umboni wamphamvu woti Akhristufe sitikhala mbali ya dziko chifukwa timafunitsitsa ndi mtima wonse kumvera lamulo lachiwiri pa malamulo akuluakulu lakuti, ‘tizikonda mnzathu mmene timadzikondera tokha.’—Mateyu 22:39.