Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 10, 2015
SOUTH KOREA

Khoti Lalikulu ku South Korea Lipereka Chigamulo pa Nkhani ya Anthu Okana Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Khoti Lalikulu ku South Korea Lipereka Chigamulo pa Nkhani ya Anthu Okana Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Pa 9 July, 2015, khoti lalikulu ku South Korea linamva maganizo a maloya okhudza dandaulo la anthu atatu amene anakana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Kodi n’chiyani chingathandize khotili kuti lizindikire kuti anthu ali ndi ufulu wokana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira? Khotili likazindikira zimenezi mwina likhoza kuthandiza dziko la South Korea kuti liyambe kupereka ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali kwa anthuwo. Vidiyoyi ikusonyeza zimene zinachitika kukhotili komanso nkhani zimene liyenera kuziganizira.