Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JUNE 28, 2018
SOUTH KOREA

Chigamulo Chosaiwalika cha Khoti Loona Zamalamulo ku Korea: Kukakamiza Anthu Kulowa Ntchito ya Usilikali N’kosemphana Ndi Malamulo

Chigamulo Chosaiwalika cha Khoti Loona Zamalamulo ku Korea: Kukakamiza Anthu Kulowa Ntchito ya Usilikali N’kosemphana Ndi Malamulo

Pa 28 June, 2018, kwa nthawi yoyamba m’mbiri ya dziko la South Korea, Khoti Loona Zamalamulo linagamula kuti chigawo china cha Malamulo a Ntchito ya Usilikali ku Korea, n’chosemphana ndi malamulo a dzikolo popeza chigawochi sichilola kuti anthu okana kulowa ntchito ya usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo azipatsidwa ntchito zina. Chigamulo chosaiwalika chimenechi n’chofunika kwambiri chifukwa chithandiza kuti lamulo loti anthu okana kulowa ntchito ya usilikali aziikidwa m’ndende lomwe lakhala likugwira ntchito kwa zaka 65 lisinthidwe.

Kungoyambira mu 1953, abale athu oposa 19,300 anagamulidwa kuti akhale m’ndende kwa zaka zoposa 36,700 tikaziphatikiza pamodzi. Panopa chigamulo cha Khoti Loona Zamalamulo chimenechi chatsegula khomo loti Khoti Lalikulu Kwambiri ku Korea liyambe kugwiritsa ntchito chigamulochi pa milandu ina yokhudza okana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo. Komanso anthu omwe amapanga malamulo ku Korea, tsopano ayenera kukhazikitsa ntchito zina zoti anthu okana usilikali azipatsidwa ndipo akuyenera kuchita zimenezi pofika pa 31 December, 2019.

Tikusangalala limodzi ndi abale athu ku Korea popeza pali chiyembekezo choti zinthu zopanda chilungamo zomwe akumana nazo kwa zaka zambiri zitha tsopano.—Miyambo 15:30.