DECEMBER 12, 2014
SOUTH KOREA
Zokhudza Misonkhano ya Mayiko: A Mboni Anatulutsa Baibulo pa Bwalo la Masewera a Mpira wa Padziko Lonse ku Seoul
SEOUL—Pa September 6 mpaka 8, 2014, a Mboni za Yehova m’dziko la Korea anachita msonkhano wa mayiko womwe unali ndi mutu wakuti, “Pitirizani Kufunafuna Ufumu wa Mulungu Choyamba.” Pa msonkhanowu a Mboni anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika m’Chikoreya. Baibuloli analimasulira kuchokera ku Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la Chingelezi, lomwe analikonzanso. Msonkhanowu unachitikira m’bwalo la masewera a mpira wa padziko lonse ku Seoul. Anthu 56,867 amene anasonkhana m’bwaloli analandira Mabaibulowa kwaulere kuphatikizaponso anthu okwana 59,091 amene ankamvetsera komanso kuonera msonkhanowu kudzera pa TV m’madera monga Busan, Daejeon, Gwangju, Jeju, Suwon ndi Yeosu. Munthu wina dzina lake Joon-yeong Choi yemwe anali pa msonkhanowu anati: “Chinthu chosaiwalika pamsokhanowu chinali kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lomwe analikonzanso.”
A Mboni ochokera ku Canada, Finland, Philippines, Poland ndiponso ku United States anapita ku Seoul kukachita nawo msonkhanowu. A Dae-il Hong omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Korea anati: “Tinakonzekera mwakhama msonkhano wosangalatsa komanso wophunzitsawu ndipo zinthu zayenda bwino kwambiri kuposa mmene tinkayembekezera. Tinganene kuti unali mwayi wapadera kuchitira msonkhanowu kuno.”
Anthu amene anasonkhana m’bwalo lamasewera la Seoul, anasangalala kwambiri ataona Mabaibulo akuluakulu atatu omwe anaikidwa ngati zokongoletsera pa bwaloli. Koma pambuyo pake anaona kuti Mabaibulowa ndi malo obatiziramo. Anthu 630 anabatizidwa pa malowa ndipo enanso okwana 596 anabatizidwa m’malo ena amene ankamvetsera msonkhanowu kudzera pa TV moti onse obatizidwa analipo 1,226.
Lankhulani ndi:
Kuchokera M’mayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000
Republic of Korea: Dae-il Hong, tel. +82 31 690 0033