Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

AUGUST 30, 2018
SOUTH KOREA

Khoti Lalikulu Kwambiri ku South Korea Linamvetsera Maganizo a Oweruza Osiyanasiyana pa Mlandu wa Anthu Okana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Chikhulupiriro Chawo

Khoti Lalikulu Kwambiri ku South Korea Linamvetsera Maganizo a Oweruza Osiyanasiyana pa Mlandu wa Anthu Okana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Chikhulupiriro Chawo

Lachinayi pa 30 August, 2018, oweruza onse a Khoti Lalikulu Kwambiri ku South Korea, anapezekapo pa nthawi yozenga milandu ya a Mboni za Yehova atatu omwe anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Anthuwa anakambirana kwa nthawi yaitali zokhudza nkhanza zomwe dziko la Korea lakhala likuchitira anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo ndipo oweruza onse okwana 13 anafunsa mafunso maloya oimira Mboni za Yehova ndi anthu enanso kwa maola 4. Kenako oweruza anakambirana kwa nthawi yaitali zokhudza chigamulo chosaiwalika chomwe Khoti Lalikulu Loona za Malamulo linapanga pa 28 June, 2018, kuti nyumba ya malamulo ikhazikitse lamulo loti anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha chikhulupiriro chawo azikhala ndi ufulu wosankha ntchito zina m’malo mowamanga ngati kuti apalamula mlandu. Maloya oimira Mboni za Yehova anapempha khoti kuti ligamule kuti abale athu atatu alibe mlandu ndipo chigamulochi chithandiza makhoti ang’onoang’ono poweruza milandu yoposa 900 yomwe akuyembekezera kuzenga. Panopa Khoti Lalikulu Kwambiri likufunika kusankha kuti ligamula liti nkhani yokhudza abale atatuwa komanso kuti ligamula zotani.

Tonsefe limodzi ndi abale athu okhulupirika oposa 100 amene adakali m’ndende tidzapitiriza kuyembekezera moleza mtima kwa Mulungu wa chipulumutso chathu.—Mika 7:7.