Pitani ku nkhani yake

Khoti Loona za Malamulo ku South Korea likuweruza mlandu pa 9 July, 2015

20 DECEMBER, 2016
SOUTH KOREA

Posachedwapa Khoti Loona za Malamulo ku South Korea Litulutsa Chigamulo Chofunika Kwambiri

Posachedwapa Khoti Loona za Malamulo ku South Korea Litulutsa Chigamulo Chofunika Kwambiri

Khoti Loona za Malamulo ku South Korea likuyembekezeka kudzapereka chigamulo chake pambuyo poti launikanso malamulo a dzikolo, pofuna kuona ngatidi kuli koyenera kuti anthu omwe amakana kulowa usilikali chifukwa cha zomwe amakhulupirira, akufunika kulangidwa. Malamulo a ntchito ya usilikali m’dzikolo amanena kuti munthu amene wakana usilikali azipatsidwa chilango. Mu July 2015 anthu ambiri anafunsidwa maganizo awo pa nkhaniyi ndipo pano ali ndi chidwi kuti nkhaniyi itha bwanji. Posachedwa a Han-chul Park omwe ndi pulezidenti wa khotili, anatsimikizira anthu kuti chigamulochi chidzaperekedwa iwowo asanachoke paudindo wawo. A Han-chul Park akuyembekezeka kudzatula pansi udindo wawo ngati pulezidenti wa khotili pa 30 January, 2017.

Chigamulo cha Khotili Chidzakhudza Anthu Ambiri

Khoti Loona za Malamulo ku South Korea ndi khoti lalikulu kwambiri lomwe linapatsidwa mphamvu yoonetsetsa kuti malamulo a m’dzikolo akutsatiridwa. Khotili linauzidwa kuti liunikenso malamulo okhudzana ndi ntchito ya usilikali omwe amanena kuti munthu akakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira kuchipembedzo chake, aziponyedwa m’ndende. Khotili likuyembekezeka kuona ngati chilango chomwe chimaperekedwa kwa anthuwa chikugwirizana kapena kutsutsana ndi malamulo oyendetsera dziko la South Korea. Malamulo oyendetsera dziko la South Korea amanena kuti munthu azikhala ndi ufulu pa nkhani zachipembedzo komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi chikumbumtima chake.

Ngati Khotili linganene kuti zimene dzikoli lakhala likuchita poika m’ndende anthu okana kulowa usilikali n’zosemphana ndi malamulo oyendetsera dzikolo, ndiye kuti boma la South Korea liyenera kuonanso bwino nkhanza zomwe lakhala likuchitira anthuwa. Ndipo ngati zingafike pamenepo ndiye kuti bomali lisiya kuimba mlandu komanso kumanga achinyamata omwe amakana kulowa usilikali chifukwa cha zomwe amakhulupirira.

Nkhani za Malamulo Sizikuyenda Bwino

M’mbuyomo, Khoti Loona za Malamuloli linaunikaponso nkhaniyi mu 2004 komanso mu 2011. M’nthawi ziwiri zonsezi, khotili linagamula kuti kulanga anthu okana usilikali, ndi kovomerezeka ndi malamulo oyendetsera dzikolo. Zimenezi zinachitikanso mu 2004 komanso mu 2007 pomwe Khoti Lalikulu Kwambiri ku South Korea komanso khoti la apilo linanena kuti nkhani ya chikumbumtima siingakhale chifukwa chomveka choti munthu n’kukanira kulowa usilikali. Ngakhale makhotiwa ananena zimenezi lamuloli limaonekabe kukhala lovuta kulitsatira ndipo nkhani yake sikutha m’makhoti.

Zikuoneka kuti makhoti a ku South Korea zikuwavuta kugamula ngati kulidi koyenera kuti munthu wokana usilikali chifukwa cha zomwe amakhulupirira aziikidwa m’ndende. Kuchokera mu 2011 pamene Khoti Loona za Malamulo linagamula za nkhaniyi, khotili linavomereza kuweruza milandu 7 yochokera ku makhoti a m’maboma osiyanasiyana komanso milandu ina 22 yomwe anthu anakasuma paokha. Anthu ena sanakhutire ndi zigamulo zimene Khoti Lalikulu Kwambiri m’dzikolo linapereka ndipo pali milandu ina yopitirira 40 ya anthu okana usilikali yomwe ikudikira kuweruzidwa ndi Khoti Loona za Malamuloli. Kuyambira mu 2015, makhoti ang’onoang’ono anagamula milandu 9 ya mtunduwu ndipo pa milandu yonseyo anagamula kuti anthu okana usilikali chifukwa cha zomwe amakhulupirira, ndi osalakwa ndipo alibe mlandu.

Mu October 2016, khoti la apilo linaona mmene makhoti aang’ono ndi akuluakulu amavutikira kuweruza nkhani zoterezi ndipo linanena kuti: “Kugwiritsa ntchito malamulo pa mlandu wa munthu wokana usilikali kukuoneka kuti ndi kovuta komanso kosokoneza.” Milandu yoyambirira ya mtunduwu yomwe khotili linagamula, linapeza kuti anthu atatu okana usilikali chifukwa cha zomwe amakhulupirira ndi osalakwa. Bungwe la Seoul Bar linasangalala kwambiri ndi chigamulo chomwe khotili linapereka ndipo linanena kuti imeneyi ndi “nkhani yosaiwalika.” A Han-kyu Kim omwe ndi pulezidenti wa bungweli ananena kuti tsopano nkhani ili m’manja mwa Khoti Loona za Malamulo kuti lipereke chigamulo chake chomaliza.

Pamene khoti la ku Gwangju linkaweruza mlandu wa a Lak-hoon Cho pa 18 October 2016, linanena kuti: “Kugwiritsa ntchito malamulo pa mlandu wa munthu wokana usilikali kukuoneka kuti ndi kovuta komanso kosokoneza.”

Posachedwa Timva za Chigamulo pa Nkhani Yomwe Yatenga Nthawi Yaitali

A Kim ananenanso kuti: “Anthu onse akudikira chigamulo chomveka bwino chomwe Khoti Loona za Malamulo lipereke. Anthu okana usilikali amazunzidwa kwambiri ndipo sapatsidwa mwayi wogwira ntchito zina m’malo mwa usilikali. Tikufuna kuti Khoti Loona za Malamulo lipereke chigamulo pa nkhaniyi mwamsanga. Anthu onse akuyembekezera kuti khotili lidzachita zinthu zosonyeza kulemekeza ufulu wa anthu.”

Kwa zaka 60 zapitazi, pafupifupi banja lililonse la Mboni za Yehova ku South Korea, lakhala likukhudzidwa ndi nkhaniyi. Azibambo komanso ana aamuna akhala akuponyedwa m’ndende chifukwa chokana ntchito yausilikali. Ngati khoti lingagamule kuti anthuwa ali ndi ufulu, ndiye kuti nkhanza zonse zomwe achinyamata akukumana nazo zitha komanso akhala ndi ufulu pa nkhani zachipembedzo komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene amakhulupirira.

Aliyense akuyembekezera mwachidwi chigamulo chomwe Khoti Loona za Malamulo lipereke.