Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

SOUTH KOREA

Kodi Dziko la South Korea Liyamba Kulemekeza Ufulu wa Anthu Wochita Zinthu Mogwirizana ndi Zimene Amakhulupirira?

Kodi Dziko la South Korea Liyamba Kulemekeza Ufulu wa Anthu Wochita Zinthu Mogwirizana ndi Zimene Amakhulupirira?

Bambo Seon-hyeok Kim omwe ali ndi zaka 28 ndipo ali ndi mkazi komanso ana, akulimbana ndi vuto lalikulu kwambiri pa moyo wawo. Chakumayambiriro kwa 2015, bambowa anazengedwa mlandu kukhoti wokana ntchito yausilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Potengera malamulo amene mayiko ambiri amatsatira, khoti la m’chigawo cha Gwangju linagamula kuti bambo Kim ndi wosalakwa. Chigamulo choterechi chinali chachilendo m’dziko la South Korea chifukwa chakuti kwa zaka zambiri, anthu masauzande ambiri amene amakana ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira akhala akumangidwa n’kuikidwa m’ndende. Choncho, khoti la apilo linasintha chigamulochi ndipo linalamula kuti bambo Kim akakhale m’ndende miyezi 18. Koma iwo anachita apilo nkhaniyi ku Khoti Lalikulu Kwambiri la ku South Korea lomwe likuyembekezeka kuzenganso mlanduwu.

M’zaka zaposachedwapa, pakhala pali kusemphana maganizo kwambiri pakati pa anthu a m’dziko la South Korea pa nkhani yoti dzikoli limakana kupatsa anthu ufulu wochita zinthu mogwirizana ndi zimene amakhulupirira. M’dzikoli muli oweruza milandu ena amene amayesetsa kutsatira malamulo amene mayiko ambiri amayendera pa nkhaniyi. Koma zimene amagamula zimatsutsidwa ndi makhoti a apilo.

Khoti Laling’ono Linalemekeza Ufulu Wochita Zinthu Mogwirizana ndi Zimene Munthu Amakhulupirira

Pa 12 May, 2015, a Chang-seok Choi a khoti la chigawo cha Gwangju anagamula kuti bambo Kim ndi wosalakwa pa mlandu womwe ankazengedwa wokana ntchito ya usilikali. A Choi ananena kuti bambo Kim sankazemba ntchito ya usilikaliyo. M’malo mwake iwo anati bambowa, omwe ndi a Mboni za Yehova, amakonda Mulungu kwambiri ndipo zimene amakhulupirira sizikuwalola kuti azigwira ntchito ya usilikali. Ananenanso kuti bambo Kim anali wokonzeka kugwira ntchito ina iliyonse yosakhudzana ndi usilikali. a

Popereka chigamulo chake, bambo Choi ananena kuti a Kim ankachita zinthu mogwirizana ndi ufulu wawo. A Choi ananena kuti “mwa njira iliyonse ufulu wochita zinthu mogwirizana ndi zimene munthu amakhulupirira uyenera kutetezedwa.” Molimba mtima, iwo analemekeza zimene a Kim ankaona kuti ndi zoyenera. Zimene a Choi anagamulazi zinali zosemphana ndi zimene malamulo a dziko lawo amanena pa nkhaniyi koma zinali zogwirizana ndi malamulo amene mayiko ambiri amayendera pa nkhani zoterezi.

Woweruza milandu wa khoti la chigawo cha Gwangju, a Chang-seok Choi ananena kuti: “Mwa njira iliyonse ufulu wochita zinthu mogwirizana ndi zimene munthu amakhulupirira uyenera kutetezedwa, ndipo kuchita zimenezi ndi kosavuta popanda kupeputsa ntchito yoteteza dziko.”

Komiti Yoona za Ufulu wa Anthu ya Bungwe la United Nations inadzudzula dziko la South Korea popereka chilango kwa anthu amene anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Boma la South Korea linachita zimenezi m’nkhani zosiyanasiyana zokwana 5 zomwe zinakhudza anthu oposa 500. Pa zimene dziko la South Korea lachita posachedwapa, Komiti yoona za ufulu wa anthuyi inanena kuti kumangidwa kwa anthuwa ndi kosemphana ndi Gawo 9 la Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale. b Komitiyi komanso mabungwe ena analimbikitsa dziko la South Korea kuti likhazikitse lamulo loti anthu amene sakufuna kugwira ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, azipatsidwa ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali. M’chaka cha 1990 dziko la South Korea linagwirizana ndi mfundo zomwe zili mu Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale. Linavomerezanso kuti nzika za m’dzikoli zikhoza kumakatula madandaulo awo ku Komiti Yoona za Ufulu wa Anthu ya Bungwe la United Nations ngati dzikoli laphwanya ufulu wawo. Koma ngakhale kuti linanena zimenezi, dzikolo likukana kutsatira mfundozi.

Kodi ndi Wolakwa Kapena ndi Wosalakwa?

Woimira boma pamilandu anapempha khoti la apilo kuti lisinthe chigamulo chimene chinaperekedwa kwa bambo Kim, ponena kuti kukana kugwira ntchito ya usilikali kukuika pangozi chitetezo cha dzikolo. c Pa 26 November, 2015, khoti la apilo linasinthadi chigamulo chimene khoti laling’ono linapereka ndipo linanena kuti bambo Kim ndi wolakwa chifukwa chokana ntchito ya usilikali. Khotili linalamula a Kim kuti akakhale m’ndende miyezi 18.

Ngakhale kuti khoti la apilolo likudziwa zimene Komiti Yoona za Ufulu wa Anthu ya Bungwe la United Nations inanena, ilo linanena kuti malamulo amene mayiko ambiri amayendera ndi achikale. Mwansanga, bambo Kim anapanga apilo nkhaniyi ku Khoti Lalikulu komanso anapereka dandaulo lawo ku gulu lina loona za anthu omangidwa popanda zifukwa zomveka la bungwe la United Nations. d Panopa akungoyembekezera zimene a khotili komanso gululi anene.

A Khoti Lalikulu Kwambiri komanso a Khoti Loona Nkhani Zamalamulo Oyendetsera Dziko ku South Korea, akhala akukana mfundo yoti munthu ali ndi ufulu wokana ntchito ya usilikali malinga ndi zimene amakhulupirira. Mu 2004 komanso mu 2011, Khoti Loona Nkhani Zamalamulo Oyendetsera Dziko linapeza kuti malamulo oyendetsera dzikolo amanena kuti mwamuna aliyense ayenera kuphunzira usilikali. Panopa khotili likuwunika nkhaniyi kachitatu kuti lione ngati malamulo oyendetsera dzikolo amanenadi kuti mwamuna aliyense ayenera kuphunzira usilikali ndipo likuyembekezeka kupereka chigamulo chake posachedwapa.

Kuyambira mu 1953, makhoti a dziko la South Korea alamula a Mboni oposa 18,000 kuti akakhale m’ndende chifukwa chokana ntchito ya usilikali.

Kodi Dziko la South Korea Liyamba Kutsatira Malamulo Amene Mayiko Ambiri Amayendera?

Ngati Khoti Lalikulu Kwambiri lingakane apilo ya bambo Kim, zipangitsa kuti iwo aikidwe m’ndende. Bambo Kim akuda nkhawa kuti ngati angamangidwe n’kuikidwa m’ndende kwa miyezi 18, anthu a m’banja lawo asokonezeka maganizo komanso azivutika kuti apeze ndalama. Mkazi wawo ndi amene akhale ndi ntchito yosamalira ana awo awiri aang’ono. Komanso akadzatulutsidwa m’ndende, zidzakhala zovuta kwambiri kuti adzapeze ntchito chifukwa adzakhala ndi mbiri yoti anamangidwapo.

A Mboni za Yehova akuyamikira kwambiri mayiko omwe ali ndi malamulo olemekeza ufulu wa anthu amene sakufuna kugwira ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Bambo Seon-hyeok Kim komanso a Mboni za Yehova onse m’dziko la South Korea, akuyembekezera zimene makhoti agamule pa nkhani imeneyi. Kodi a Khoti Lalikulu Kwambiri komanso a Khoti Loona Nkhani Zamalamulo Oyendetsera Dziko atsatira malamulo amene mayiko ambiri amayendera zomwenso iwo analonjeza ndi mtima wonse kuti adzazitsatira? Nanga kodi dziko la South Korea liyamba kuona ufulu umene anthu ali nawo wokana ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira monga wofunika kwambiri kwa nzika zake?

a Mu 2015, khoti la chigawo cha Gwangju linagamula kuti a Mboni ena atatu ndi osalakwa. Nalonso khoti la chigawo cha Suwon linanena kuti a Mboni ena awiri ndi osalakwa pa mlandu woti ankazemba ntchito ya usilikali.

b Communication No. 2179/2012, U.N. Doc. CCPR/C/112/D/2179/2012, January 14, 2015

c Woimira boma pa milandu ananena kuti kukana ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene munthu amakhulupirira kungasokoneze chitetezo cha dziko. Komabe, akatswiri ena a zamalamulo sakugwirizana ndi zimenezi. Mwachitsanzo, a Gwan-gu Kim omwe ndi woweruza milandu pa khoti la chigawo cha Changwon Masan ananena kuti: “Palibe umboni uliwonse wosonyeza kuti kupereka ntchito zina kwa anthu amene sakufuna kugwira ntchito ya usilikali kungaike chitetezo cha dziko pachiopsezo.”

d Gulu lina loona za anthu omangidwa popanda zifukwa zomveka la bungwe la United Nations lili ndi dongosolo loti munthu akhoza kupanga apilo kuti athandizidwe. Izi zingachitike ngati chifukwa chimene amumangiracho komanso kumusunga zikuphwanya ufulu wake woperekedwa ndi malamulo amene mayiko ambiri amayendera.