Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MAY 7, 2018
SOUTH KOREA

A Mboni za Yehova Anagwira Ntchito Yapadera Yogawira Mabuku Pampikisano wa 2018 wa Olimpiki Komanso wa Anthu Olumala

A Mboni za Yehova Anagwira Ntchito Yapadera Yogawira Mabuku Pampikisano wa 2018 wa Olimpiki Komanso wa Anthu Olumala

Kuyambira pa 9 mpaka 25 February 2018, ndi pa 9 mpaka 18 March, 2018, ku Pyeongchang kunachitika Mpikisano wa 2018 wa Olimpiki Komanso wa Anthu Olumala. Abale ndi alongo a ku Korea anagwira ntchito yapadera yomwe inathandiza kuti alendo ochokera m’mayiko osiyanasiyana apeze mabuku ofotokoza Baibulo kwaulere.

Abale ndi alongo oposa 7,100 ochokera m’madera osiyanasiyana m’dzikolo anagwira nawo ntchitoyi. Ambiri mwa abale ndi alongowa anali ochokera m’mizinda ya Busan, Gwangju, Incheon, Seoul, komanso Suwon ndipo ena anachokera ku chilumba cha Jeju komwe ndi kutali kwambiri. Chilumbachi chili pamtunda wa makilomita 500 kum’mwera kwa dera la Pyeongchang ndipo alendo ambiri odzaona malo amakonda kupitako.

Abale ndi alongowa anaika mashelefu amateyala okwana 152 m’malo 48 kuphatikizapo bwalo la mpikisano wa Olimpiki la Gangneung komanso la Pyeongchang. Analoledwanso kuika mabuku awo ena pakhomo lolowera malo ena ogona anthu (Olympic Village) kumenenso kumachitika zokhudza chipembedzo.

Mashelefu amateyala awiri pafupi ndi khomo lolowera m’bwalo la mpikisano wa Olimpiki la Gangneung.

Kuwonjezera pamenepa, akuluakulu a ku Gangneung anapereka chilolezo choti mashelefu amateyala aikidwe pa siteshoni yatsopano ya sitima zothamanga kwambiri zodutsa m’njanji ya KTX Gyeonggang, zomwe zimanyamula anthu kuchokera ku Incheon ndi ku Seoul kupita nawo ku Pyeongchang. Anthu oposa 28,000, anadutsa pa siteshoni ya Gangneung patsiku lotsegulira Masewera a Olimpiki.

Pofuna kuthandiza alendo pafupifupi 80,000 ochokera m’mayiko ena, abale athu anagawira mabuku, timabuku, magazini ndi timapepala. Zimene anagawirazi zinali za zilankhulo 20 monga Chitchainizi, Chingelezi, Chikazaki, Chikoreya ndi Chirasha. Komanso, abale ndi alongo olankhula bwino Chinenero Chamanja cha ku Korea anagwiritsa ntchito mashelefu amateyala omwe ankasonyezapo mavidiyo a chinenero chamanja pofuna kulandira anthu ambiri a vuto losamva omwe anabwera ku Mpikisano wa Anthu Olumala. Abale ndi alongowa anagawira timabuku ndi mabuku oposa 71,200.

A Mboni za Yehova padziko lonse amagwiritsa ntchito mashelefu amateyala oposa 300,000 pofuna kusonyeza anthu mabuku komanso zinthu zina m’mayiko oposa 35. Njira imeneyi imawathandiza kuti athe kulalikira anthu kulikonse kumene angapezeke komanso kuti akwaniritse mbali zonse za utumiki wawo.—2 Timoteyo 4:5.