Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JUNE 16, 2014
SOUTH KOREA

Oweruza Milandu Akuvutika Maganizo Poweruza Anthu Okana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Oweruza Milandu Akuvutika Maganizo Poweruza Anthu Okana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Woweruza milandu wina kukhoti laling’ono m’dera la Suwon analira pamene ankawerenga chigamulo chomwe chinaperekedwa kwa mnyamata wina wazaka 21, dzina lake Chang-jo Im, yemwe anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Ngakhale kuti patsikuli woweruza milanduyo anali ataweruza milandu ina 5 popanda kumva chisoni, iye analira powerenga chigamulo cha mlandu wa mnyamatayu chifukwa mlanduwu unaweruzidwa mopanda chilungamo. Popeza woweruzayo sakanatha kuchitira mwina, iye anapereka chigamulo chakuti mnyamatayo, yemwe ndi wa Mboni za Yehova, akakhale kundende kwa miyezi 18.

Mwezi uliwonse, oweruza milandu a m’dziko la South Korea amafunika kuweruza milandu ngati imeneyi. Pa mlanduwu, Chang-jo Im anafotokoza kuti sangalowe usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Ngakhale kuti mnyamatayu sanafunikire kuikidwa m’ndende, mayi yemwe ankaweruza mlanduwu anapereka chigamulo chakuti akakhale kundende kwa miyezi 18. Woweruza winanso dzina lake Young-sik Kim, anafotokoza maganizo ake pa nkhani yoweruza anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Iye anati: “Sikuti oweruza amaona kuti ‘akukhaulitsa zigawenga’ akamapereka chilango kwa anthu amene amakana kulowa usilikali.” Zimenezi zinachititsa woweruzayo kuyamba kuona kuti malamulo oweruzira milandu ya anthu okana kulowa usilikali m’dzikoli ali ndi vuto.

Boma la South Korea likupitiriza kukana zoti munthu ali ndi ufulu wokana kulowa usilikali ndipo bomali silinaike ntchito iliyonse yoti munthu angasankhe kugwira ngati sakufuna kulowa usilikali. Izi zikuchititsa kuti oweruza milandu a m’dzikoli azivutika maganizo akamapereka chigamulo choti anthu amene akana kulowa usilikali atsekeredwe m’ndende ngati zigawenga. Oweruzawa akudziwanso kuti nthambi ya bungwe la UN Yoona za Ufulu Wachibadwidwe yakhala ikudzudzula boma la South Korea kuti likuphwanya ufulu wachibadwidwe wa anyamata 501 a m’dzikoli omwe akukana kulowa usilikali, powaimba milandu komanso kuwamanga ngati zigawenga. Nthambi ya bungweli ikudzudzula dzikoli chifukwa likuphwanya mfundo zimene mayiko onse anagwirizana, zoti azilemekeza ufulu wachibadwidwe wa nzika za m’mayiko awo, womwe ndi wofunika kwambiri. Choncho n’zosadabwitsa kuti oweruza milandu ochuluka m’dzikoli amamva chisoni kwambiri akamapereka chigamulo choti anyamata achikhristu amene akana kulowa usilikali amangidwe ngati zigawenga.

Panopa, pali milandu ina imene yatumizidwa kukhoti lalikulu m’dziko la South Korea, kuchokera kumakhoti ang’onoang’ono m’dzikoli. Milanduyi yatumizidwa kukhoti lalikululi ndi oweruza 6 a kumakhoti ang’onoang’ono, ndipo ikukhudza anthu omwe akana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Oweruzawo achita zimenezi ngakhale kuti chaposachedwapa mu 2011, khoti lalikululi linalengeza zoti malamulo a dzikolo amati munthu aliyense wamwamuna akufunika kuphunzira usilikali. Potumiza milanduyi kukhoti lalikululi, oweruzawo anaperekanso madandaulo amene anthu ali nawo pa nkhani yolowa usilikaliyi.

Zimene oweruza ena anena . . .

  • Kodi anthu omwe akana kumenya nkhondo chifukwa cha zimene amakhulupirira, akuyeneradi kumangidwa?

    “Malamulo a dziko lino akuyenera kuteteza ufulu wa nzika zake, monga ufulu woti munthu azikhulupirira zimene iyeyo akufuna. Ufulu umenewu ndi wofunika kwambiri, ndipo munthu aliyense amaona kuti iyeyo ndi wofunika komanso akulemekezedwa ngati ufuluwu ukulemekezedwa. . . . Ngakhale kuti anthu ambiri m’dzikoli sakugwirizana n’zoti anthu ena azikana kuphunzira usilikali, sizingakhale zoona kunena kuti anthu omwe akukana kuphunzira usilikali apalamula mlandu woopsa, wosafunira zabwino dziko lawo ndipo akufunika kupatsidwa chilango chokhwima ngati chimene chimaperekedwa kwa zigawenga.”—Woweruza Hye-won Lim, wa kukhoti laling’ono la Suwon, February 21, 2013, 2012Chogi2381.

    “Chinthu chofunika kwambiri chimene chimathandiza munthu kuti akhale ndi khalidwe labwino, ndi kukumbukira zoti iyeyo amafunikira anthu ena kuti zinthu zimuyendere bwino . . . komanso kuganizira zoti ‘munthu aliyense ndi wofunika kwambiri.’ Kukumbukira zimenezi kumathandiza munthu kuti azilemekeza ena, ndipo sangachotse moyo wa anzake ngakhale pa nthawi ya nkhondo. Ngati anthu amene asankha kutsatira mfundo zimenezi akukakamizidwa kuti aphunzire usilikali kapena kuti amenye nkhondo, ndipo akupatsidwa chilango chifukwa chokana kuchita zimenezi, ndiye kuti ufulu wawo ukuphwanyidwa komanso sakulemekezedwa.”—Woweruza Young-hoon Kang, wa kukhoti lina laling’ono kumpoto kwa mzinda wa Seoul, January 14, 2013, 2012Chogi1554.

  • Kodi kulemekeza ufulu umene munthu ali nawo wokana kulowa usilikali kungasokoneze chitetezo m’dziko?

    “Palibe umboni wolembedwa kapena wodalirika wosonyeza kuti ngati boma litakhazikitsa ntchito zina zoti anthu amene akana kulowa usilikali azigwira, ndiye kuti chitetezo cha dziko chingasokonezeke kapena zingasokoneze ntchito yophunzitsa anthu usilikali.”—Woweruza Gwan-gu Kim, wa kukhoti laling’ono la Changwon Masan, August 9, 2012, 2012Chogi8.

    “Palibe chifukwa chomveka chosalemekezera ufulu wa anthu onse m’dziko lino, ngakhalenso ufulu wa anthu ena ochepa, monga a Mboni za Yehova, . . . amene akukana kuphunzira usilikali ndiponso kumenya nkhondo. Zimene anthuwa asankha kuchita sizingasokoneze chitetezo cha dziko lino ngakhale pang’ono. Ndipotu anthuwa . . . akukana kulowa usilikali ngakhale kuti akumapatsidwa chilango. Zikanakhala kuti n’zoonadi kuti anthu amene akukana kuphunzira usilikali angachititse kuti chitetezo cha dziko chisokonezeke, ndiye kuti tikananena zoti panopa chitetezo cha dzikoli chasokonezeka kale komanso ufulu wa anthu onse m’dzikoli wasokonezedwa.—Woweruza Seung-yeop Lee, wa kukhoti laling’ono la Ulsan, August 27, 2013, 2013Godan601.

  • Kodi nkhaniyi ingathetsedwe bwanji?

    “Ngati khoti lalikulu litagamula kuti zimene zikuchitika pozenga milandu a Mboni za Yehova chifukwa chokana kulowa usilikali n’zosagwirizana ndi malamulo a dziko lino, ndiye kuti ofesi ya pulezidenti ndi nduna zake komanso nyumba ya malamulo, ingathe kuunikanso malamulo okhudza chitetezo cha dziko lino komanso ufulu umene munthu aliyense ali nawo wokana kuphunzira usilikali. Akamaunika nkhani zimenezi, angathe kukonzanso malamulowo kuti azilemekeza ufulu umene munthu aliyense ali nawo komanso kuti chitetezo cha dziko lino chisasokonezeke.”—Woweruza Young-sik Kim, wa kukhoti laling’ono la kum’mwera kwa mzinda wa Seoul, July 9, 2013, 2013Chogi641.

    “Chiwerengero cha asilikali a dziko lino sichingatsike komanso chitetezo sichingasokonezeke ngati boma litakhazikitsa ndondomeko yabwino yoti anthu amene akukana kuphunzira usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, azigwira ntchito zina zoyenerera. Zimenezi zingathandizenso kuti pasapezeke anthu amene angapezerepo mwayi n’kumazemba kulowa usilikali ponamizira kuti ndi a Mboni za Yehova.”—Woweruza Seong-bok Lee, woweruza wa kukhoti laling’ono la kum’mawa kwa mzinda wa Seoul, February 20, 2014, 2014Chogi30.

Kodi khoti lalikulu lichita chiyani?

Oweruzawa apempha khoti lalikululi kuti lipereke chigamulo chake pa nkhani yomwe ikuwasowetsa mtendereyi, yokhudza milandu ya anthu omwe akukana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Panopa, khoti lalikululi lagamula milandu 29 mokomera anthu a Mboni za Yehova, ndipo pa milanduyi pali milandu iwiri yokhudza anthu 433 a Mboni.

Kodi khoti lalikulu ku South Korea lipereka chigamulo chotani pa milanduyi? Kodi khotili lilemekeza ufulu umene anthu ali nawo wokana kulowa usilikali, zomwe zingachititse kuti malamulo a dzikoli akonzedwenso? Ngati khotili lingachite zimenezi, ndiye kuti lilemekeza mfundo zimene mayiko onse amayendera, zimene khotili linavomereza kutsatira. Komanso khotili likachita zimenezi lilemekezanso malamulo a dzikoli komanso lisonyeza kuti likulemekeza ufulu wa anthu ena, zomwe zingachititse kuti anyamata ambirimbiri omwe akumangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali, apeze mpumulo.