Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 27, 2015
SOUTH KOREA

A Mboni a ku Korea Anapereka Madandaulo Awo ku Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka

A Mboni a ku Korea Anapereka Madandaulo Awo ku Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka

M’mwezi wa July ndi August 2015, anyamata oposa 600 a ku South Korea anapereka madandaulo awo ku Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka. Aliyense mwa anthuwa anaimbidwa mlandu wokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira ndipo anaweruzidwa kuti ndi wolakwa n’kugamulidwa kuti akakhale m’ndende miyezi 18.

Chimene Chinachititsa Kuti Apereke Madandaulo

Pa 15 October 2014 Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu inapeza kuti dziko la South Korea lili ndi mlandu womanga anthu popanda zifukwa zomveka. Dzikoli linali litamanga anthu amene anakana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Anyamatawo anatumiza madandaulo awo ku gulu lija chifukwa mpaka pano dziko la South Korea likumangabe anthu amene amakana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

Ntchito imene Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka imagwira ndi “yofufuza nkhani zokhudza kuphwanyira anthu ufulu wawo popanda zifukwa zomveka kapena mosagwirizana ndi . . . mfundo zimene mayiko ambiri amayendera zomwe dzikolo linavomereza.”

Loya woimira anthu odandaulawo, dzina lake Du-jin Oh, anafotokoza chifukwa chake ndi zosamveka kumanga anthu okana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

Mayiko onse amafunika kuti azipereka mwayi wa ntchito zamtundu wina kwa anthu awo amene sakufuna kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Izi zili choncho chifukwa kukana usilikali chifukwa cha zimene munthu amakhulupirira kukugwirizana ndi ufulu wachipembedzo komanso wotsatira zimene umakhulupirira. Koma dziko la South Korea likupitirizabe kukana kupereka ntchito zina kwa anthu okana usilikali ngakhale kuti mayiko ena akulipempha kuchita zimenezi.

Aliyense akhoza kuona kuti zimene dziko la South Korea likuchita ndi zosamveka. Dzikoli likukana kuthetsa nkhani imene inayamba zaka 60 zapitazo ndipo yakhudza anthu oposa 18,000 ndiponso mabanja awo. Boma lalephera kupeza njira yothandizira anyamatawo mogwirizana ndi zimene komiti ija yakhala ikulipempha kuchita kwa maulendo 5. N’zoonekeratu kuti si chilungamo kumanga anthu ngati kuti ndi zigawenga chifukwa choti akukana kuvulaza anthu ena.

Zimene Anapempha Kuti Gululo Lichite

Anyamata a ku South Korea amene anapereka madandaulo awo akupempha kuti gulu la United Nations liwathandize:

  • “Potsimikizira kuti zimene boma linachita powamanga chifukwa choti anakana kulowa usilikali chifukwa chotsatira zimene amakhulupirira ndi zosamveka.”

  • “Polamula dziko la South Korea kuti limasule mwamsanga anthu odandaulawo ndiponso lichotse mayina awo m’kaundula wa anthu amene anapalamulapo mlandu.”

Anamangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Mnyamata wina amene anamangidwa ndipo anapereka nawo dandaulo lake ndi Jun-hyeok An. Mofanana ndi odandaula enawo, iye sakuona kuti ali ndi mlandu. Kuyambira ali mwana, mayi ake anamuphunzitsa kuti adziwe ndiponso azitsatira mfundo za m’Baibulo. Iye anasankha yekha kuti sangalowe usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. a Podziwa zimene zimachitikira munthu m’dziko la South Korea akakana kulowa usilikali, iye anaiganizira nkhaniyi mofatsa n’kusankhiratu zimene angachite. Iye anati:

Ndikuona kuti sindiyenera kumangidwa chifukwa chotsatira zimene ndimakhulupirira. Ngati boma likanandipatsa mwayi wogwira ntchito yamtundu wina ndikanavomera. Koma ndikuona kuti palibe chifukwa chomveka chondilangira chifukwa choti ndikukana kuvulaza anthu ena.

Kodi Boma la South Korea Lidzasintha?

Gulu la United Nations lija litumiza madandaulo okwana 631 ku boma la South Korea kuti linene maganizo ake pa nkhaniyi. Boma likachita zimenezi, gululi lidzauza nthambi ya United Nations yoona za ufulu wa anthu zimene lapeza komanso zimene likuona kuti ziyenera kuchitika. Nthambiyi ikavomera kuti palibe zifukwa zomveka zoti anthu omwe akana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira azimangidwa, ndiye kuti boma la South Korea lidzudzulidwa kwambiri chifukwa chophwanya ufulu wa anthu ake. A Du-jin Oh ananenanso kuti:

Mpaka pano, dziko la South Korea likukanabe kukhazikitsa malamulo oti anthu okana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira akhoza kumagwira ntchito zamtundu wina. Dzikoli likukanabe ngakhale kuti mayiko ambiri akulipempha kuchita zimenezi. Nawonso makhoti a m’dzikoli akusonyeza kuti akufunanso kuti boma lisinthe pa nkhaniyi. M’miyezi yapitayi, oweruza a makhoti awiri agamula kuti anthu okwana 6, omwe anakana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, ndi osalakwa. Kuyambira mu 2012, oweruza ena anakasuma milandu 7 kukhoti lalikulu la m’dzikoli ndipo mu July 2015, khotili linamva zimene maloya ananena pa nkhaniyi.

Panopa, boma la South Korea likuchita zotsutsana ndi mfundo zimene mayiko ena amayendera chifukwa likupitiriza kumanga a Mboni okwana 40 kapena 50 mwezi uliwonse. Jun-hyeok An ndiponso a Mboni ena omwe anamangidwa chifukwa chokana usilikali ku South Korea akudikirira zimene nthambi ya United Nations ija ndiponso khoti lalikulu la ku South Korea lingagamule pa nkhaniyi.