Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

FEBRUARY 19, 2015
SOUTH KOREA

Dziko la South Korea Lapezeka ndi Mlandu Womanga Anthu Okana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Dziko la South Korea Lapezeka ndi Mlandu Womanga Anthu Okana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Komiti Yoona za Ufulu Wachibadwidwe ya Bungwe la United Nations inadzudzula dziko la South Korea chifukwa chophwanya ufulu wa a Mboni wotsatira zimene amakhulupirira ndiponso kuwamanga chifukwa chokana kulowa usilikali. Aka ndi ka nambala 5 kuti komitiyi idzudzule dziko la South Korea. Kameneka n’koyamba kuti khotili linene kuti kumangidwa kwa a Mboniku n’kosemphana ndi malamulo amene mayiko a m’bungweli amatsatira. a

Pa maulendo 4 amene komitiyi inadzudzula dziko la South Korea, pa milandu yokhudza a Mboni 501 amene anakana kulowa usilikali, komitiyi inapeza kuti dziko la South Korea linaphwanyira anthuwa ufulu wochita zimene munthu akuganiza, ufulu wotsatira zimene amakhulupirira ndiponso ufulu wa chipembedzo. Zimenezi zili m’gawo 18 la Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale. Pa October 15, 2014 ndi pamene komitiyi inapanga chigamulo ndipo inalengeza chigamulochi pa January 14, 2015. Chigamulochi chinkakhudza anyamata 50 a Mboni b. Komitiyi inapeza kuti zimene dziko la South Korea linachita pomanga anyamatawa kunali kuwaphwanyira ufulu wawo ndipo dzikoli linaphwanya gawo 9 la Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale. Panganoli limaletsa kumanga anthu popanda zifukwa zomveka ndipo limanena kuti munthu ayenera kupatsidwa chipukuta misozi akamangidwa mopanda chilungamo. Komitiyi inanenanso kuti kumanga munthu mopanda chilungamo komanso mosatsatira malamulo n’kosaloleka. Choncho komitiyi inagamula kuti: “Mogwirizana ndi gawo 18 la panganoli, n’kulakwa kumanga anthu chifukwa choti akutsatira zimene amakhulupirira malinga ndi chipembedzo chawo.”

Dziko la South Korea Lalamulidwa Kuti Lithetse Mlanduwu

Mu chigamulo chimene Komitiyi inapereka, inanena kuti dziko la South Korea lifufute mbiri yoti a Mboni 50 anamangidwapo komanso lipereke chipukuta misozi kwa a Mboniwa. Inanenanso kuti “boma la dzikoli likufunika . . . kukonzanso malamulo ake kuti aziteteza anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.” Komitiyi inanenanso kuti masiku 180 asanathe kuchokera pamene inapereka chigamulochi, dziko la South Korea likhale “litanena zimene lachita pofuna kusonyeza kuti likutsatira zimene komitiyi yagamula.”

Kwa nthawi yaitali dziko la South Korea lakhala likukana kupereka ntchito zina kwa anthu amene akana kulowa usilikali, chifukwa choopa kuti zimenezi zisokoneza chitetezo cha dzikolo, ndiponso anthu ambiri m’dzikolo samagwirizana ndi zoti anthu okana kulowa usilikali azipatsidwa ntchito zina. Koma komitiyi inanena kuti zifukwazi ndi zosamveka ndipo uwu ndi ulendo wa nambala 5 kuti komitiyi ikane zifukwazi. Mu 2006, dziko la South Korea linaperekanso zifukwa zofananazi ndipo komitiyi inakana. Poona zifukwa zimene dzikoli linapereka, komitiyi inanena kuti dziko la South Korea “lalephera kunena mavuto enieni amene angabwerepo ngati litamalemekeza ufulu wa anthu amene akana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.” Pa nkhani yokhudza kubweretsa bata ndi mtendere, komitiyi inanena kuti “kulemekeza ufulu wa anthu amene akana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira n’kumene kungathandize kuti anthu azikhala mwa bata ndi mtendere.” Komitiyi ikunenetsa kuti dziko la South Korea lilibe zifukwa zomveka zomangira anthu okana kulowa usilikali chifukwa chotsatira zimene amakhulupirira.

Zimene dziko la South Korea likuchita pomanga anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, zikusonyezeratu kuti likuchita zinthu zosemphana ndi malamulo amene mayiko ambiri amayendera okhudza nkhaniyi.

Ngakhale kuti dziko la South Korea linalowa m’Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale mu 1990, dzikoli lakhala likukana kwamtu wagalu kutsatira malamulo okhudza anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Ndipotu chaka chilichonse anyamata ambiri a Mboni amamangidwa ku South Korea. Komiti Yoona za Ufulu Wachibadwidwe ya Bungwe la United Nations yakhala ikunena mobwerezabwereza kuti dziko la South Korea likulakwa kumanga a Mboni. Sitikukayikira kuti nthawi ifika ndithu pamene dzikoli liyambe kuchita zimene mayiko ambiri akuliuza ndiponso kukhazikitsa malamulo olemekeza ufulu wa nzika za dzikolo.

a Onani CCPR Communication No. 2179/2012, Mlandu wapakati pa Young-kwan Kim et al. v. Republic of Korea, Zimene zinalembedwa m’panganoli anagwirizana pa October 15, 2014 ndipo zikupezeka mu ndime 7.5.

b Chithunzi chimene chili pamwambapa chikusonyeza anyamata 30 pa anyamata 50 a Mboni amene ankaimbidwa mlandu ndipo aima kutsogolo kwa khoti lalikulu la ku South Korea komwe anachita apilo yoyamba.