Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

DECEMBER 9, 2013
SOUTH KOREA

Dziko la South Korea Lasiya Kuphatikiza Anthu Omangidwa pa Nkhani Zokhudza Chikumbumtima Chawo ndi Akaidi Ena Onse

Dziko la South Korea Lasiya Kuphatikiza Anthu Omangidwa pa Nkhani Zokhudza Chikumbumtima Chawo ndi Akaidi Ena Onse

Dziko la South Korea lachepetsako mavuto a anthu ambirimbiri a Mboni za Yehova amene ali kundende chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira. Dzikoli lachepetsa mavutowa polola kuti anthu a Mboni asamaphatikizidwe ndi akaidi ena.

Izi zatheka chifukwa cha msonkhano umene anthu oimira Mboni za Yehova ku Korea anachita ndi mkulu wa boma woyang’anira ndende ku Korea. Msonkhanowu unachitika mu December 2012, ndipo panalinso bambo wina wa Mboni yemwe mwana wake wamwamuna ali kundende. Pa msonkhanowu a Mboni anadandaula kuti anyamata a Mboni nthawi zambiri amaikidwa m’zipinda limodzi ndi akaidi oopsa kwambiri. Patangodutsa miyezi pafupifupi 5 chichitikireni msonkhanowu, anyamata a Mboni oposa 70 analekanitsidwa ndi akaidi ena ndipo anaikidwa m’zipinda limodzi ndi a Mboni anzawo.

A Mboni akhala akumangidwa kwa nthawi yaitali chifukwa chokana kulowa usilikali. Dziko la South Korea lakhala likumanga anthu a Mboni za Yehova kwa nthawi yaitali chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amaphunzira m’Baibulo. Pakali pano, anthu a Mboni pafupifupi 600 ali kundende chifukwa chokana kuchita zinthu zosemphana ndi chikumbumtima chawo. Zaka zoposa 60 zapitazi, anthu a mboni oposa 17,000 akhalapo kundende chifukwa chokana kulowa usilikali. M’dzikoli anakhazikitsa lamulo lakuti munthu aliyense wamwamuna wazaka za pakati pa 19 ndi 35 azilowa usilikali.

Moti sizachilendo kuti mabanja a Mboni za Yehova a mibadwo yosiyanasiyana anazunzidwapo, kuimbidwa mlandu komanso kutsekeredwa m’ndende ngati zigawenga. Mnyamata wina wa Mboni za Yehova dzina lake Seungkuk Noh anatulutsidwa kundende mu 2000 pambuyo pokhalako zaka zitatu. Iye ananena kuti: “Ndinalamulidwa kukakhala kundende imene bambo anga anakhalakonso ali mnyamata ndipo moyo wakundendeko sunasinthe kuyambira nthawi imeneyo mpaka pano.” Masiku ano munthu amene amamangidwa chifukwa chotsatira chikumbumtima chake amayenera kukhala kundende miyezi 18 ndipo dziko la South Korea silinakhazikitsebe ntchito zina zoti anthu okana kulowa usilikali azigwira.

Bambo Ho Gyu Kang anatumizidwa kundende ali ndi zaka 21 chifukwa chokana kulowa usilikali. Aka kanali koyamba pa moyo wawo kusiyana ndi makolo awo. Bambo Kang ananena kuti: “Ndinkachita mantha kwambiri.” Iwo pamodzi ndi anyamata ena a Mboni anaikidwa malo amodzi ndi akaidi ena amene anali oopsa kwambiri. Ena mwa akaidiwa anali oti anapha anthu ndipo ena anali m’gulu la zigawenga zoba ndi mfuti.

Kwa nthawi yonse imene amakhala kundende, a Mboni za Yehova amazunzidwa kwambiri m’njira zosiyanasiyana ndi akaidi ena. Vuto lina limakhala lakuti Mboniwa omwe nthawi zambiri amakhala anyamata, amaikidwa m’zipinda zomwe muli akaidi akuluakulu. Akaidiwa amachitira nkhanza akaidi a Mboni ndipo zimenezi zimawalepheretsa kuchita zinthu zokhudza kulambira kwawo monga kupemphera komanso kuphunzira Baibulo paokha. Kwa zaka zambirimbiri, anyamata a Mboni akhala akuzunzika ndi zinthu zochititsa manyazi komanso zowachotsera ulemu zimene akaidi ena ankawachitira.

Lamulo losiyanitsa akaidi likugwirizana ndi malamulo amene mayiko ambiri amayendera. Zimene dziko la South Korea layamba kuchitazi ndi zogwirizana ndi mfundo zosiyanasiyana zimene mayiko ambiri amayendera pa nkhani yokhudza akaidi. Imodzi mwa mfundozi imapezeka pa Gawo 8 la Malamulo a Bungwe la United Nations a Zimene Akaidi Ayenera Kuchitiridwa. Apa dziko la South Korea lachita zogwirizana ndi zimene dziko la Greece, lomwe ndi membala wa bungwe la European Union, linachita zaka 20 zapitazo. Pa nthawiyi, Unduna wa Zachitetezo cha M’dziko ndi Chilungamo unavomereza kuti a Mboni za Yehova omangidwa chifukwa cha chikumbumtima chawo azisiyanitsidwa ndi akaidi ena. M’chaka cha 1992, Unduna wa Zachitetezo unasintha kampu ya ku Sindos, m’dera la Thessalonica, kuti ikhale malo a Mboni za Yehova basi. Lipoti lina lochokera kuboma linanena kuti “Unduna wa Zachitetezo wachita zinthu zoganizira athu a Mboni za Yehova chifukwa kunena zoona anthuwa sikuti ndi zigawenga,” ndipo zithandiza kuti a Mboni azikhala malo osiyana ndi akaidi ena. Mu 1998, dziko la Greece linasiya kumanga a Mboni amene ankakana kuchita zinthu zosiyana ndi chikumbumtima chawo.

Nalonso dziko la South Korea lachita zinthu zoganizira anyamata a Mboni za Yehova powasiyanitsa ndi akaidi ena. Anyamatawa amamangidwa osati chifukwa chakuti ndi zigawenga koma chifukwa chotsatira mwakufuna kwawo zimene amaphunzira m’Baibulo. a Anthu oyang’anira ndende zosiyanasiyana komwe kuli a Mboni za Yehova ambiri atsatira lamulo losiyanitsa a Mboni ndi akaidi ena ndipo izi zathandiza kuti anthu omangidwa chifukwa chotsatira chikumbumtima chawowa azikhala motetezeka. Mnyamata wina wa Mboni yemwe ndi mkaidi kundende yotchedwa Gunsan anayamikira kwambiri chifukwa chosiyanitsidwa ndi akaidi ena. Iye anati: “Panopa ndife otetezeka ku makhalidwe oipa monga kugonana komanso kalankhulidwe koipa. Timasangalala kukambirana nkhani zolimbikitsa ndi a Mboni anzathu.”

‘Panopa ndife otetezeka ku makhalidwe oipa ndipo tikusangalala kumakambirana nkhani zolimbikitsa ndi a Mboni anzathu.’

Dziko la South Korea silikulemekezabe ufulu wa anthu okana kulowa usilikali. Ngakhale kuti zimene dziko la South Korea likuchita posiyanitsa a Mboni ndi akaidi ena n’zabwino, komabe dzikoli silikutsatirabe zimene mayiko ena akuchita pothetsa nkhani yokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene munthu amakhulupirira. Mwachitsanzo kuyambira chaka cha 1997, dziko la Greece linayamba kumapereka ntchito zina kwa anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Dzikonso la Germany poyamba linkapereka ntchito zina kwa anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Koma kungoyambira m’chaka cha 2011 dzikoli linasiya kukakamiza anthu amene akana kulowa usilikali, kuti azigwira ntchito zina. Nalonso dziko la Taiwan kuyambira m’chaka cha 2000 linakhazikitsa lamulo lopereka ntchito zina kwa anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

Achinyamata a Mboni komanso mabanja awo akukhulupirira kuti dziko la South Korea liyamba kutsatira malamulo amene mayiko ambiri padziko lonse amayendera amene amalemekeza ufulu wachibadwidwe wa anthu pa nkhani ya zimene munthu amakhulupirira.

a Malamulo a mayiko onse amene Dziko la South Korea liyenera kumayendera amafotokoza kuti kukana kulowa usilikali chifukwa cha zimene munthu amakhulupirira ndi ufulu wachibadwidwe wa munthu. Kuti mumve zambiri pa nkhaniyi werengani nkhani yakuti “Mayiko ndi Mabungwe Akudzudzula Dziko la South Korea Chifukwa cha Zinthu Zopanda Chilungamo Zimene Likuchita.”