Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

19 OCTOBER 2016
SOUTH KOREA

Khoti la Apilo ku South Korea Lapeza Kuti Anthu Omwe Amakana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira ndi Osalakwa

Khoti la Apilo ku South Korea Lapeza Kuti Anthu Omwe Amakana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira ndi Osalakwa

Pa 18 October 2016, khoti la apilo la m’boma la Gwangju linagamula kuti anthu atatu: A Hye-min Kim, a Lak-hoon Cho ndi a Hyeong-geun Kim, omwe anakana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira, ndi osalakwa. Anthu atatuwa ndi a Mboni za Yehova ndipo ndi oyamba kupezeka osalakwa pa mlandu ngati umenewu m’khoti la apilo ku South Korea.

A Young-sik Kim omwe ankaweruza mlanduwu ananena kuti: “Khoti lapeza kuti anthuwa anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira m’chipembedzo chawo komanso chifukwa cha chikumbumtima chawo. Malamulo a dziko lino amalemekeza ufulu wachipembedzo wa munthu komanso chikumbumtima chake. Choncho palibe amene angapatsidwe chilango chifukwa chotsatira zimenezi.”

Ngati loya wa boma angachite apilo pa chigamulochi, ndiye kuti mlanduwu uyenera kupita ku Khoti Lalikulu kuti akaonenso. Palinso milandu ina yoposa 40 yofanana ndi mlanduwu yomwe anthu ake anagamulidwa kuti ndi olakwa ndipo ikudikira kuti ionedwenso ndi khoti lalikulu. A Philip Brumley omwe amaimira a Mboni za Yehova pa nkhani za malamulo ananena kuti: “Khoti la apiloli laona kuti anthuwa ali ndi ufulu wokana ntchito ya usilikali potsatira zimene mayiko anagwirizana pa nkhaniyi, ngakhale kuti mpaka pano Khoti Lalikulu komanso Khoti Loona za Malamulo Oyendetsera Dziko ku South Korea limakana kuti anthuwo ali ndi ufulu. Chigamulo chimene khoti la apilo linapereka ndi cholondola chifukwa Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu inaweruzapo milandu ngati imeneyi yoposa 500, ndipo inagamula kuti anthu omwe amakana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira ndi osalakwa.”