Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Khoti Loona za Malamulo Oyendetsera Dziko la South Korea pa tsiku limene linapanga chigamulo chosaiwalikachi.

JULY 13, 2018
SOUTH KOREA

Kuchitira Chilungamo Anthu Okana Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira ku South Korea: Chigamulo Chomwe Anthu Akhala Akuchiyembekezera kwa Nthawi Yaitali

Kuchitira Chilungamo Anthu Okana Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira ku South Korea: Chigamulo Chomwe Anthu Akhala Akuchiyembekezera kwa Nthawi Yaitali

Kwa zaka 65, Akhristu achinyamata m’dziko la South Korea akhala akuikidwa m’ndende chifukwa chokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Koma Lachinayi pa 28 June, 2018, Khoti Loona za Malamulo Oyendetsera Dziko linapereka chigamulo chosaiwalika chomwe chinasintha zomwe dzikoli lakhala likuchita. Khotili linagamula kuti Gawo 5 ndime 1 mu Malamulo a Ntchito ya Usilikali si logwirizana ndi malamulo oyendetsera dzikolo, chifukwa boma la South Korea silinapereke mwayi woti anthu akhoza kusankha kugwira ntchito zina m’malo mwa usilikali.

Atolankhani ali panja pa khoti. Atolankhani a mayiko osiyanasiyana ankatsatira mwachidwi mlanduwu.

Pa nthawiyi, oweruza 9 ndi amene anakambirana za nkhaniyi ndipo tcheyamani anali mkulu wa oweruza milandu a Lee Jin-sung. Pa oweruza 9 amenewa, 6 anagwirizana ndi chigamulo chatsopanochi chomwe n’chogwirizana kwambiri ndi mfundo zimene mayiko ambiri akuyendera omwe amalemekeza ufulu woganiza, wokhulupirira zimene munthu akufuna, komanso wosankha zinthu mogwirizana ndi chikumbumtima.

Oimira Mboni za Yehova ku Korea ali mkati mwa khoti kudikirira chigamulo cha khotilo.

Pa chaka, chiwerengero cha anthu omwe boma la South Korea limawamanga chifukwa chokana usilikali, chimaposa chiwerengero cha mayiko ena onse kuchiphatikiza pamodzi. Pa nthawi ina, abale athu okwana 500 mpaka 600 ankamangidwa chaka chilichonse pa avereji. Ndipo akawatulutsa, abale athuwa ankakhala ndi mbiri yoti anapalamulapo mlandu zomwe zinkachititsa kuti azikumana ndi mavuto osiyanasiyana kuphatikizapo kuvutika kuti apeze mwayi wa ntchito.

Komabe, kuyambira mu 2011, abale ena anayamba kudandaula za nkhaniyi ku Khoti Loona za Malamulo Oyendetsera Dziko chifukwa Malamulo a Ntchito ya Usilikali, sankapereka ufulu woti anthu omwe akana kulowa usilikali azipatsidwa ntchito zina, koma kungowamanga basi. Komanso kuyambira mu 2012, oweruza milandu ena amene sankagwirizana ndi zoti anthu okana usilikali azipatsidwa chilango, anaganiza zopititsa milandu ya anthuwo ku Khoti Loona za Malamulo Oyendetsera Dziko kuti liunikenso Malamulo a Ntchito ya Usilikali.

A Hong Dae-il omwe amayankhula m’malo mwa a Mboni za Yehova ku Korea, akufunsidwa mafunso kunja kwa khoti pambuyo poti khotilo lapereka chigamulo chake

Udindo wa Khoti Loona za Malamulo Oyendetsera Dziko ku Korea ndi kuonetsetsa ngati lamulo lililonse likugwirizana ndi malamulo oyendetsera dzikolo kapena ayi. Mu 2004 ndi mu 2011, khotili linapereka chigamulo chogwirizana ndi lamulo loti mwamuna aliyense azigwira ntchito ya usilikali, koma panopa lavomereza kuti mpofunika kusintha lamuloli. Khotili linauza boma la South Korea kuti lilembenso lamuloli ndipo liphatikizemo mfundo yoti munthu amene sakufuna usilikali azipatsidwa ntchito zina. Khotili linanena kuti boma liyenera kuchita zimenezi pofika kumapeto kwa chaka cha 2019. Ntchito zina zomwe anthu okana usilikali angamapatsidwe ndi monga kugwira ntchito kuchipatala, komanso ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali zomwe cholinga chake n’kuthandiza anthu a m’madera awo.

Pofotokoza kufunika kwa chigamulo chimene khotili linapanga, M’bale Hong Dae-il yemwe amalankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku Korea anati: “Khoti Loona za Malamulo Oyendetsera Dziko ndi khoti lamphamvu kwambiri m’dzikoli lomwe timateteza maufulu a anthu ndipo zomwe lachitazi zithandiza kuti nkhaniyi ithetsedwe. Abale athu akuyembekezera mwachidwi kugwira ntchito zothandiza madera lawo zomwe sizikutsutsana ndi zimene amakhulupirira ndipotu zimenezi n’zimenenso zikuchitika m’mayiko ambiri.”

Pali nkhani zinanso zofunika zimene zikuyembekezera kuthetsedwa, kuphatikizapo nkhani zokhudza a Mboni 192 amene anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali, komanso milandu 900 yomwe ikuyembekezera kuzengedwa ndi makhoti osiyanasiyana.

Zimene Khoti Loona za Malamulo Oyendetsera Dziko linanenazi zithandiza kuti Khoti Lalikulu Kwambiri lizigamula mokomera anthu amene sakufuna kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Zimene oweruza onse a Khoti Lalikulu Kwambiri angagamule zikhudza mmene makhoti amene akuzenga milandu ya anthu okana usilikali angaweruzire mlandu uliwonse.

Pa 30 August, 2018 Khoti Lalikulu Kwambiri lidzakambirana za nkhaniyi ndipo kenako lidzapereka chigamulo chake. Aka kakhala koyamba pambuyo pa zaka 14 kuti oweruza onse a Khoti Lalikulu Kwambiri aunike ndi kukambirananso nkhani ya anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

Panopa aphungu a nyumba yamalamulo ku Korea ali mkati mosintha Malamulo a Ntchito ya Usilikali.

M’bale Mark Sanderson wa m’Bungwe Lolamulira anati: “Tikuyembekezera mwachidwi chigamulo chimene Khoti Lalikulu Kwambiri lipereke. Abale athu a ku Korea analolela kuvutika podziwa kuti ‘zili bwino ngati wina chifukwa cha chikumbumtima chake kwa Mulungu, akupirira zowawa ndi kuvutika popanda mlandu.’ (1 Petulo 2:19) Ndipo tikusangalala nawo limodzi chifukwa khoti lavomereza kuti abalewa akhala akuchitidwa zinthu zopanda chilungamo, komanso chifukwa choti anali olimba mtima pochita zinthu zogwirizana ndi chikumbumtima chawo.”