MAY 27, 2020
SPAIN
Kalata Yoyamikira Yochokera kwa Nesi Wina ku Spain
Pamene kuli mliri wa kolonavairasi, abale ndi alongo ambiri akuyetsetsa kulimbikitsa anzawo powalembera makalata. M’bale Josué Laporta ndi mkazi wake Vanesa, analembera makalata olimbikitsa anthu ogwira ntchito ndiponso odwala matenda a COVID-19 pachipatala china mumzinda wa Barcelona ku Spain. Nesi wina anayankha kalata yawo. Onani kalatayi m’munsimu ndipo yasinthidwa mwina ndi mwina titapatsidwa chilolezo chake. a
Ndine nesi . . ndipo ndikulemba kalatayi m’malo mwa [dzina lachotsedwa] omwe ndi agogo aakazi azaka 97. Tinawawerengera kalata yanu lero m’mawa. Ndikukhulupirira kuti sindinalandire kalatayi mwangozi ngakhale kuti tikalandira makalata, timangowapereka kwa wodwala aliyense mosasankha. Kalatayi yathandiza ineyo ndi [wodwalayu] . . . , kuti tikhale ndi chiyembekezo. [Munthuyu] akudwala mwakayakaya ndiye anandiuza kuti akufuna kukufunsani funso asanachoke padzikoli. Funso lake ndi lakuti: “Ngakhale kuti ndili ndi zaka 97, kodi ndingathe kudzaona malonjezo omwe analembedwa m’Baibulo akukwaniritsidwa?”
M’mawawu ndinamuwerengera pang’ono nkhani ya pawebusaiti yomwe munatumiza ija kwa 10 minitsi. Nkhaniyo inamukhudza kwambiri moti nkhope yake inasintha ndipo anayamba kuoneka wosangalala. Sindinamuonepo akuoneka choncho. Kenako ndinaonera naye vidiyo yakuti, “N’chifukwa Chiyani Yesu Anafa?”
Ndinawerenganso magazini ya [“Galamukani!”] yosonyeza zimene tingachite kuti tichepetse nkhawa. Yandithandiza kuti ndizipirira mavuto amene tikukumana nawo panopa. Monga mmene mukudziwira, zinthu sizili bwino.
Pachipatala pano tilibe akatswiri otithandiza tikakhala ndi nkhawa, komabe nthawi iliyonse tikumawerenga uthenga womwe mwatipatsawu ndiponso tikumaganizira za uthenga umenewu. Mliriwu ukadzatha, ndikufunitsitsa kudzaphunzira zambiri. Ndikukhulupirira kuti mudzapitiriza kundiphunzitsa kuti ndidziwe zinthu zondithandiza kukhulupirira kuti moyo udzakhalanso bwino padzikoli. Ndikusowa chonena. Ndikuthokoza Mulungu chifukwa choti kalata yanu inangofika pa nthawi yake. Nditailandira ndinakaisiya m’chipinda mwa [wodwala].
Ndikukhulupirira kuti nonse muli bwino ndiponso sindikukayikira kuti zimene mumakhulupirira zimakuthandizani kupirira mavuto omwe tikukumana nawo panopa kuposa mmene enafe timachitira. Zikomo kwambiri chifukwa chopatula nthawi yanu pothandiza ineyo ndi [wodwalayu]. Mwatithandiza kwambiri kuti tipeze mtendere kwa milungu 6 yapitayi ndipo munachita zimenezi ngakhale kuti simukutidziwa.
Ndikukuthokozani kuchokera pansi pamtima.
Tikamamva zinthu zolimbikitsa ngati zimenezi, zimatichititsa kupitirizabe kulalikira pamene kuli mliri woopsawu. Tikupemphera kuti anthu azilimbikitsidwa akamva mawu otonthoza amene timagwiritsa ntchito polalikira.—Miyambo 15:23.
a Kalatayi inalembedwa m’Chisipanishi.