Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Abale ali m’mphepete mwa msewu kudikirira kuti akwere galimoto kupita kumalo achitetezo

JANUARY 2, 2024
SUDAN

Abale Ndi Alongo Akakamizika Kuthawanso Nkhondo ku Sudan

Abale Ndi Alongo Akakamizika Kuthawanso Nkhondo ku Sudan

Abale anyamula Mkhristu mnzawo yemwe wadwala pa nthawi imene amathawa ku Wad Madani

Pa 15 December 2023, nkhondo ya pakati pa magulu awiri ku Khartoum, lomwe ndi likulu la dziko la Sudan inafalikira mumzinda winanso wotchedwa Wad Madani. Malinga ndi nkhani ina yomwe inatuluka pa jw.org, nkhondoyi itayamba ku Khartoum mu April 2023, abale ndi alongo ambiri anathawira mumzinda wa Wad Madani, womwe uli pa mtunda wa makilomita 170, kum’mawa chakummwera kwa mzinda wa Khartoum. Panopa abale ndi alongo oposa 150 akakamizikanso kuthawa zachiwawa zimene zikuchitika mumzindawu.

Mmene Nkhondoyi Yakhudzira Abale ndi Alongo

  • Palibe m’bale kapena mlongo amene wavulala kapenanso kuphedwa

  • Pafupifupi abale ndi alongo 158 akusowa pokhala. Ena athawira m’mizinda ndi m’mayiko ena

  • Abale ndi alongo okwanira 10 komanso achibale awo omwe si Mboni adakali mumzinda wa Wad Madani

Ntchito Yopereka Chithandizo

  • Oyang’anira madera komanso akulu akugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo polimbikitsa abale ndi alongo amene akhudzidwa

  • Makomiti Othandiza Pakachitika Ngozi Zamwadzidzidzi ku Sudan ndi mayiko oyandikana nawo, akupitiriza kuyendetsa ntchito yopereka chithandizo ndi zinthu zina zofunikira monga chakudya, mankhwala ndi malo okhala

Anthu 7 omwe anabatizidwa ku Wad Madani kutatsala masiku ochepa kuti nkhondo iyambike

N’zochititsa chidwi kuti patatsala mlungu umodzi kuti nkhondo ya mumzinda wa Wad Madani iyambike, ofesi ya nthambi ya East Africa inakonza zoti abale ndi alongo omwe anathawa nkhondo, aonere pulogalamu yojambulidwa ya msonkhano wachigawo wakuti, “Khalani Oleza Mtima” wa Chiarabu. Pa anthu pafupifupi 200 amene anapezeka pamsonkhanowu, 145 anali abale ndi alongo omwe anathawa nkhondo kuchokera ku Khartoum. Anthu ambiri omwe anapezeka pamsonkhanowu anathokoza kwambiri chifukwa cha zimene anaphunzira. Mbali imene inawalimbikitsa kwambiri inali vidiyo ya sewere yamutu wakuti “Muzilola Kuti Yehova Akutsogolereni,” imene inafotokoza zinthu zofanana ndi zimene zinawachitikira. Anthu 7 anabatizidwa pamsonkhanowu.

Ndi pemphero lathu kuti abale ndi alongo athu ku Sudan apitirize kupirira mayesero amenewa ndipo tikuyembekezera nthawi imene Yehova ‘adzathetsa nkhondo padziko lonse lapansi.’​—Salimo 46:9.