NOVEMBER 18, 2020
TAJIKISTAN
M’bale Jovidon Bobojonov Wakhululukidwa Ndi Pulezidenti wa ku Tajikistan Ndipo Watulutsidwa M’ndende
M’bale Jovidon Bobojonov atatulutsidwa m’ndende pa 1 November 2020 ananena kuti: “Yehova anandithandiza kukhalabe ndi chikhulupiriro cholimba.” Pa 31 October 2020, Pulezidenti wa ku Tajikistan anakhululukira Jovidon ndi akaidi ena 377. Jovidon anagwira ukaidi kwa miyezi 9 yokha pa zaka ziwiri zomwe anagamulidwa kuti akhale m’ndende chifukwa chokana usilikali potsatira zimene amakhulupirira.
Pa 4 October 2019, asilikali anapita kunyumba kwa Jovidon amene pa nthawiyo anali ndi zaka 19 n’kupita naye kukamusunga ku ofesi imene amalemba anthu usilikali. Kwa miyezi ingapo anamusamutsira kumalo osiyanasiyana komwe kumakhala asilikali. Kumalo onsewa ankamufunsa chifukwa chimene anakanira kulowa usilikali ndipo ankafunika kuyankha mafunso omweomwewo. Jovidon anafotokoza kuti: “Akuluakulu a asilikali ndi asilikali ena ambirimbiri ankandifunsa mafunso osamveka ndipo cholinga chawo chinali choti ndisiye kukhala wa Mboni. Anayesetsa ndithu kundipanikiza ndi mafunso n’cholinga choti ndikwiye. Nthawi zina ankandidzutsa ndikugona n’kumandifunsanso mafunso onse omwe anandifunsa kale maulendo angapo kuti ndifotokoze chifukwa chimene ndinakanira kulowa usilikali.”
Jovidon anafotokozanso kuti: “Pemphero linandithandiza kwambiri. Masana ndi usiku ndinkapemphera mochokera pansi pa mtima kwinaku ndikulira ndipo ndinkapempha Yehova kuti andithandize kupirira, kuti ndisamukhumudwitse komanso ndisayankhe chilichonse anthuwa akamandipsetsa mtima.”
“Yehova anagwira dzanja langa mwamphamvu . . . Ndikamva kuti ndili ndekhandekha ndinkavutika maganizo. Koma Yehova ankandilimbikitsa ndi kundipatsa mphamvu pogwiritsa ntchito zinthu zimene analenga. Ndikadzuka m’mawa uliwonse ndinkamva kaphokoso ka mbalame zikuimba. Usiku ndinkayang’ana mwezi ndi nyenyezi. Mphatso zochokera kwa Yehova zimenezi zinkandithandiza kukhala wosangalala ndiponso zinkandilimbikitsa.”
Pa 2 April 2020, khoti linagamula kuti Jovidon ndi wolakwa ndipo linamusamutsa kuchoka kumalo kumene anamusunga kuja n’kupita naye kundende. Sankaloledwa kulandira makalata. Komabe, abale ndi alongo ankamubweretsera chakudya ndipo ankalemba mawu a lemba la tsiku pazikwama zomwe aikamo zakudyazo. Jovidon anati: “Zimenezi zinandithandiza kwambiri kuti ndisadzimve ngati ndili ndekhandekha ndipo ndinazindikira kuti anzanga amandikonda kwambiri.”
Jovidon anasangalala kwambiri kuti ankakumbukiranso malemba olimbikitsa monga Aroma 8:37-39. Iye anati: “Pa nthawi yomwe ndinali m’ndende ndinazindikira kuti mawu apalembali ndi oona. Palibe mayesero amene anatha kundilekanitsa ndi chikondi cha Yehova. Yehova anandithandiza kukhalabe ndi chikhulupiriro cholimba.”
Zimene zinachitikira Jovidon zalimbikitsa kwambiri makolo ake. Bambo ake dzina lawo a Abdujamol anati: “Chikhulupiriro chathu chalimba chifukwa cha mapemphero komanso chitsanzo chabwino chimene mwana wathu anasonyeza pokhalabe wokhulupirika pamene ankalimbana ndi mayesero. Abale ndi alongo athu onse padziko lonse anatithandizanso kwambiri. Timayamikira kwambiri mapemphero awo. Tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa chotipatsa anzathu omwe amatikonda kwambiri chonchi.”
M’nthawi ya mapetoyi tonsefe tikuyembekezera kukumana ndi mayesero omwe ali ngati “moto umene ukuyaka.” (1 Petulo 4:12) Mpake kuti m’mawu ake omaliza Jovidon akunena kuti: “Popeza kuti panopa ndinamasulidwa, ndikufuna kugwiritsa ntchito ufulu umenewu popitiriza kuphunzira zambiri zokhudza Yehova ndi kukonzekera bwino mayesero omwe ndingadzakumane nawo m’tsogolo. Kwa abale ndi alongo amene simunakumanepo ndi mayesero aakulu chonchi, mukufunika kugwiritsa ntchito ufulu umene muli nawo popitiriza kuphunzira zambiri zokhudza Yehova mwa kuwerenga Mawu ake komanso mabuku athu.”