SEPTEMBER 17, 2013
TANZANIA
Khoti Lalikulu Kwambiri ku Tanzania Lateteza Ufulu Wachibadwidwe wa Ana a Sukulu a Mboni
DAR ES SALAAM, Tanzania—Pa July 12, 2013, Khoti la Apilo ku Tanzania, lomwe ndi khoti lalikulu kwambiri m’dzikolo, linapereka chigamulo chimene oweruza onse a khotili anagwirizana, chakuti sukulu za m’chigawo cha Mbeya zinaphwanya ufulu wolambira wa ana 127. Khotilo linagamula zimenezi chifukwa ena mwa anawo anachotsedwa sukulu ndipo ena anapatsidwa chilango chifukwa chokana kuimba nawo nyimbo ya fuko potsatira zimene anawo amakhulupirira.
Mu 2007, akuluakulu a sukulu ya Shikula anachotsa sukulu ana 5 a Mboni chifukwa choti anawo anakana kuimba nawo nyimbo ya fuko. Kuwonjezera pamenepa, sukulu zina za pulayimale ndi sekondale m’dera lomweli zinapereka chilango kwa ana ena 122 a Mboni chifukwanso chosaimba nawo nyimbo ya fuko. Ngakhale kuti ana onse 127 anayesetsa kudandaula nkhaniyi kwa akuluakulu oona za maphunziro komanso kwa nduna yaikulu, sizinaphule kanthu. Kenako ophunzirawo anakadandaula ku Khoti Lalikulu la ku Tanzania. Khotili lili ndi mphamvu zambiri moti limaposedwa ndi khoti limodzi lokha m’dzikolo. Koma n’zomvetsa chisoni kuti khotili linagwirizana ndi zoti anawo achotsedwe sukulu, ngakhale kuti si oweruza onse a khotili amene anagwirizana ndi chigamulochi. Poona kuti zinthu sizinayende, pa December 2, 2010, ana a sukuluwo anakadandaula nkhaniyi ku Khoti la Apilo. Malinga ndi zikalata za kukhoti, Khoti la Apilo la m’dzikolo lili ndi mphamvu kwambiri moti chigamulo chimene lingapereke chikhoza “kusintha chigamulo chilichonse” chimene makhoti ena angapereke.
Bambo Zadok Mwaipwisi, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Tanzania anati: “Tasangalala kwambiri ndi chigamulo chimene khotili lapereka ndipo zimenezi zateteza ufulu wa anawa wotsatira zimene amakhulupirira. Chigamulochi chikugwirizana ndi malamulo a dziko lino amene amapereka ufulu wolambira kwa anthu a m’dzikoli. Izi zithandizanso anthu omwe ndi nzika za dziko lino amene si a Mboni za Yehova.”
Lankhulani ndi:
Kuchokera m’mayiko ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000
Tanzania: Zadok Mwaipwisi, tel. +255 22 2650592