AUGUST 20, 2019
THAILAND
Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu Latulutsidwa M’Chilao
Pa 16 August, 2019, a Mboni za Yehova anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chilao, pa msonkhano wachigawo womwe unachitikira mumzinda wa Nong Khai ku Thailand. M’bale Plakorn Pestanyee wa m’Komiti ya Nthambi ya Thailand ndi amene anatulutsa Baibuloli pa tsiku loyamba la msonkhanowu.
Ntchito yomasulira Baibuloli inagwiridwa ndi anthu atatu ndipo anaigwira kwa chaka ndi hafu. Mmodzi mwa anthuwo anati: “Ntchitoyi yathandiza kuti tikhale ndi Baibulo lomwe uthenga wake wafotokozedwa m’njira imene anthu wamba oyankhula Chilao amayankhulira. Komabe, likufotokoza molondola tanthauzo la chinenero choyambirira chomwe chinagwiritsidwa ntchito polemba Baibulo, kuti anthu amene akuphunzira Baibuloli amvetse ‘zinthu zozama za Mulungu.’”—Yobu 11:7.
Baibuloli lili ndi zinthu zambiri zothandiza pophunzira, monga mlozera nkhani yemwe cholinga chake n’kuthandiza owerenga kupeza mavesi omwe akufuna mosavuta komanso lili ndi gawo la matanthauzo a mawu ena opezeka m’Baibulo. Munthu winanso yemwe anamasulira nawo Baibuloli anati: “Tikakagwiritsa ntchito Baibuloli pophunzitsa anthu, ophunzirawo akamvetsa mosavuta mfundo zofunika kusiyana ndi m’mbuyomu, ndipo uthenga wa m’Baibulo ukawafika pamtima ndi kuwathandiza kuyamba kukonda kwambiri Yehova.”
Tikukhulupirira kuti Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu lithandiza abale ndi alongo oyankhula Chilao kupitiriza kukhala ‘okonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.’—2 Timoteyo 3:16, 17.