Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Vokano anaphulika pafupi ndi chilumba cha Tonga. Pachilumba chonse panali phulusa lokhalokha. Ndipo madzi omwe anasefukira, anawononga kwambiri

26 JANUARY, 2022
TONGA

Vokano Komanso Madzi Osefukira Zinawononga Kwambiri ku Tonga

Vokano Komanso Madzi Osefukira Zinawononga Kwambiri ku Tonga

Pa 15 January 2022, madzi osefukira anawononga pachilumba cha Tonga. Madziwa anasefukira chifukwa cha vokano amene anaphulika pa Nyanya Yaikulu ya Pacific. Kuphulika kwa vokanoyi kunamveka ngakhale kumadera akutali monga ku South America ndi ku Japan. Phulusa lomwe linagwera m’madera ambiri komanso madzi osefukira, zinawononga dera lalikulu ku Tonga ndipo njira zofalitsira mauthenga zinasokonekera.

Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu

  • Palibe m’bale kapenanso mlongo aliyense amene wavulala

Ntchito Yopereka Chithandizo

  • Kunakhazikitsidwa Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi

  • Abale anathandiza anthu amene anakhudzidwa powachotsera phulusa pamadenga a nyumba ndi m’mapaipi olumikizana ndi denga momwe mumadutsa madzi akumwa

  • Onse omwe anathandiza nawo pantchito yopereka chithandizoyi ankatsatira njira zonse zodzitetezera ku COVID-19

Abale ayambiranso kuchita zinthu zokhudza kulambira ndipo akuchita misonkhano nthawi zonse. Tikudziwa kuti Yehova apitiriza ‘kuthandiza ndi kulimbikitsa’ abale ndi alongo athu omwe akhudzidwa ndi tsokali.​—Salimo 86:17.