Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Nyumba ya Ufumu ya ku Mersin

JUNE 3, 2016
TURKEY

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Lagamula kuti Dziko la Turkey Liyenera Kuvomereza Nyumba za Ufumu Monga “Malo Olambirira”

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Lagamula kuti Dziko la Turkey Liyenera Kuvomereza Nyumba za Ufumu Monga “Malo Olambirira”

Pa 24 May, 2016, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linapereka chigamulo chakuti anthu a m’zipembedzo zing’onozing’ono m’dziko la Turkey ali ndi ufulu wochita zinthu zokhudza zipembedzo zawo. Khotili linanenanso kuti dziko la Turkey likugwiritsa ntchito molakwa malamulo ake okhudza kugawa malo pofuna kukana kuvomereza kuti Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova ndi “malo olambirira.”

Khotili linapeza kuti malamulo a dziko la Turkey okhudza kugawa malo amavomereza nyumba zopemphereramo zomwe ndi zokulirapo koma savomereza nyumba zopemphereramo zocheperapo. Choncho, dziko la Turkey likugwiritsa ntchito malamulowa polepheretsa a Mboni m’dzikolo kuti azilambira momasuka ndipo zimene dzikolo likuchita zikusemphana ndi zomwe zili mu gawo 9 la Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya. a Chigamulo cha Khotilo chinanena kuti akuluakulu a dziko la Turkey “akugwiritsa ntchito lamulo lokhudza kugawa malo pokhazikitsa mfundo zokhwima zoti anthu a m’zipembedzo zing’onozing’ono, kuphatikizapo a Mboni za Yehova, azitsatira.”

Lamulo Lokhudza Kugawa Malo Likuchititsa Kuti Zipembedzo Zing’onozing’ono Zizivutika

Chipembedzo cha Mboni za Yehova chinalembetsa ku boma la Turkey ndipo n’chovomerezeka. Kwa zaka zambiri a Mboniwo akhala akupempha akuluakulu a boma kuti malamulo okhudza kugawa malo azivomereza Nyumba za Ufumu monga “malo olambirira”. Koma akuluakuluwo amakana kuti avomereze zimenezi.

Popeza kuti a Mboni sangathe kumanga Nyumba za Ufumu mogwirizana ndi malamulo a dziko la Turkey okhudza kugawa malo, pali nkhawa yakuti boma likhoza kutseka Nyumba za Ufumu zokwana 25 zomwe zili m’dzikolo. Akuluakulu a boma akhala akutseka Nyumba za Ufumu m’madera a Mersin ndi Akçay kuyambira mu 2003. Ku Karşıyaka m’chigawo cha İzmir, akuluakulu a boma anakana kuvomereza Nyumba ya Ufumu monga malo olambirira. Chigamulo cha Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya chimene chinaperekedwa pa 24 May chinali chokhudza Nyumba za Ufumu za ku Mersin ndi İzmir.

Chisanafike chake cha 2003, lamulo la dziko la Turkey lokhudza kugawa malo linkangokhudza kumanga mizikiti. Panthawiyi, akuluakulu a boma a m’madera osiyanasiyana anavomereza mosachita kuonetsera kuti a Mboni azisonkhana. Mu 2003 dziko la Turkey linasintha lamulo la nambala 3194 lokhudza kugawa malo pofuna kugwirizana ndi mfundo zimene mayiko a ku Ulaya amayendera zokhudza ufulu wolambira ndiponso kupewa tsankho. Mwachitsanzo, mu lamuloli pamene panali mawu akuti “mizikiti” anaikapo mawu akuti “malo olambirira.” Lamuloli linayambanso kuvomereza kuti anthu a zipembedzo zina azipatsidwa malo omangapo nyumba zopempherera.

Tinganene kuti kusinthidwa kwa lamulo lokhudza kugawa malo kumayenera kupereka ufulu kwa zipembedzo zing’onozing’ono womanga nyumba zawo zopemphereramo. Koma zimene zikuchitika n’zakuti kusinthaku kukungokomera zipembedzo zokhazo zimene zili ndi anthu ambiri komanso amene kamangidwe kawo ka nyumba zopempherera kali kogwirizana ndi zimene Asilamu amachita akamapemphera.

Kugwiritsa Ntchito Lamulo Molakwika Kukuchititsa Kuti Zipembedzo Zina Zisakhale ndi “Malo Opempherera”

Kuonjezera pamenepo, akuluakulu a m’madera osiyanasiyana sanasunge malo oti anthu a m’zipembedzo zing’onozing’ono azimangapo nyumba zopempherera ndipo amakana zimene a Mboni akhala akupempha zoti malamulo okhudza kugawa malo asinthidwe. A Mboniwa akapita kukhoti kukadandaula, a khotiwo limodzi ndi akuluakulu a boma amagwiritsabe ntchito malamulo omwewo okhudza kugawa malo pokana kuvomereza Nyumba za Ufumu za a Mboniwo monga “malo olambirira.”

Akuluakulu oyang’anira ku Mersin komanso ku Akçay, anagwiritsa ntchito lamulo latsopanoli mosayenera ndipo anatseka Nyumba za Ufumu kumeneko chifukwa akuti zinali zosavomerezeka monga “malo olambirira.” A Mboni a m’deralo atapempha ngati angapatsidwe malo ena oti azipemphererako, akuluakuluwo anawauza kuti panalibe malo ochitira zimenezo.

Zimene zinachitika m’madera awiriwa zayamba kuchitikanso m’madera ena ambiri a m’dziko la Turkey. A Mboni za Yehova komanso zipembedzo zina zomwe zili ndi anthu ochepa, akulephera kupeza chilolezo kuti malo awo olambirira azionedwa monga ovomerezeka. Pofika panopo, akuluakulu a m’madera 27 a dziko la Turkey, akana maulendo okwana 46 pempho la a Mboni loti ayambe kuvomereza malo awo olambirira. Kuonjezera pamenepo, m’dziko la Turkey malo opempherera amene ndi ovomerezeka samalipira ndalama za msonkho, magetsi kapena madzi. Koma malamulo savomereza mipingo ing’onoing’ono kuti nayonso isamalipire zinthu zimenezi.

A Mboni Anachita Apilo ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya

A Mboni asanachite apilo ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya, anali atasuma za nkhaniyi ku ma khoti onse m’dzikoli. Limodzi la makhotiwo ndi khoti lalikulu la Council of State. Khoti limeneli silinavomerepo pempho la a Mboni za Yehova lakuti malamulo a dziko la Turkey awasinthe n’cholinga chakuti Nyumba za Ufumu za a Mboni zizionedwa monga malo olambirira. Khotili linafika mpaka posintha chigamulo china chomwe chinkakomera a Mboni chimene khoti lina laling’ono linapereka.

Panopo a Mboni za Yehova apereka kale zisamani ziwiri ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya n’cholinga choti khotili liunike ngati zomwe akuchita akuluakulu a dziko la Turkey sizikusemphana ndi zomwe zili mu Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Chisamani china anachipereka mu 2010 ndipo china anachipereka mu 2012. Potengera mfundo zimene linakhazikitsa m’mbuyomu, khotili linatsindika kufunika kwa malamulo okhudza kugawa malo omwe amavomereza magulu a zipembedzo zing’onozing’ono kukhala ndi malo awoawo opemphereramo.

Khoti la ku Ulayali linanena kuti “anthu azipembedzo zing’onozing’ono monga a Mboni za Yehova sangakwanitse kuchita zinthu zomwe zili mu lamulo lokhudza kugawa malo kuti apatsidwe malo opempherera oyenera.” Khotili linanenanso kuti: “Makhoti a m’dziko la Turkey sanachite zinthu moganizira zofuna za anthu a zipembedzo zing’onozing’ono. . . . Popeza kuti alipo ochepa, a Mboni za Yehova sakufunika kuchita kukhala ndi nyumba yomangidwa mwa mtundu wina wake, koma kanyumba koti azingokumanamo n’kumalambira ndi kumaphunzitsana zinthu zimene amakhulupirira basi.”

Malinga ndi chigamulo chimene khoti la ku Ulayali linapereka, zikuonekeratu kuti zimene dziko la Turkey likuchita posavomereza Nyumba za Ufumu kuti ndi “malo olambirira,” zikulepheretsa a Mboni kuti azilambira momasuka. Bambo Ahmet Yorulmaz, omwe ndi mtsogoleri wa bungwe lomwe limaimira a Mboni ku Turkey ananena kuti: “Tikusangalala ndi zimene khoti la ku Ulayali lagamula. Tikukhulupirira kuti tsopano boma la Turkey liyamba kuona Nyumba Zathu za Ufumu monga malo olambirira ndipo lilamula akuluakulu oyang’anira madera osiyanasiyana kuti azigwiritsa ntchito bwino malamulo ogawa malo n’cholinga choti tisamavutike kukhala ndi malo olambirira. Ngati dziko la Turkey lingachite zinthu mogwirizana ndi chigamulochi ndiye kuti lingathandize kwambiri kuteteza ufulu umene anthu ali nawo wolambira.”

Kodi Dziko la Turkey Lithetsa Tsankho Lobwera Chifukwa Chosiyana Zipembedzo?

Pa zaka 10 zapitazi, zinthu zakhala zikuyenda bwino kwa a Mboni za Yehova pankhani zokhudza zamalamulo m’dziko ka Turkey. M’chaka cha 2007, akuluakulu a dziko la Turkey anavomereza chipembedzo cha a Mboni za Yehova b m’dzikolo pambuyo powakana kwa zaka 70.

A Mboni za Yehova ku Turkey akuthokoza chifukwa akuluakulu a dzikoli ayamba kutsatira ndondomeko zoyenera pofuna kuti nzika za dzikolo zikhale ndi ufulu wopembedza. A Mboniwa akukhulupirira kuti zimene agamula a khoti lalikulu la ku Ulaya posachedwapa zithandiza kuti akuluakulu a dzikoli asamaphwanye ufulu wolambira umene anthu a m’dzikolo ali nawo. M’malamulo a dziko la Turkey komanso malamulo a mayiko ena muli ufulu umenewu. A Mboniwo akuyembekezera mwachidwi kuona dziko la Turkey likuchita mogwirizana ndi zimene khoti la ku Ulaya lagamula ndiponso kuti livomereza Nyumba za Ufumu zokwana 25 zomwe zili m’dzikoli monga malo olambirira. Akukhulupiriranso kuti mtsogolo dzikoli lidzawalola kumanga nyumba zopemphereramo mogwirizana ndi kuchuluka kwa anthu awo.

a Gawo 9 limanena za “ufulu wonena maganizo ako, ufulu wotsatira zimene umakhulupirira ndiponso ufulu wopembedza.”

b Bungwe lomwe limaimira a Mboni za Yehova ku Turkey linakhazikitsidwa pa 31 July, 2007.