Pitani ku nkhani yake

MARCH 17, 2014
TURKEY

Dziko la Turkey Likukana Kutsatira Mfundo Zimene Mayiko a ku Ulaya Amayendera Zokhudza Ufulu wa Anthu

Dziko la Turkey Likukana Kutsatira Mfundo Zimene Mayiko a ku Ulaya Amayendera Zokhudza Ufulu wa Anthu

“Nzika iliyonse ya dziko lino la Turkey ndi msilikali.” Mawu amenewa ndi otchuka kwambiri m’dziko la Turkey. Mwachitsanzo, ana a sukulu amaphunzitsidwa mawuwa, akuluakulu a zipani zandale amawalankhula pamisonkhano yawo, komanso akuluakulu a asilikali amawalankhula pouza anthu amene angolowa kumene usilikali. Malamulo a m’dzikoli amakakamiza munthu aliyense wamwamuna kuti alowe usilikali akafika pa msinkhu winawake, ndipo anthu ambiri amasangalala akaitanidwa kuti aphunzire ntchito yausilikali. Choncho n’zosadabwitsa kuti boma la Turkey likukana zoti munthu ali ndi ufulu wokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira.

Dziko la Turkey lili m’gulu la mayiko ochepa kwambiri pa mayiko amene ali m’Bungwe la Mayiko a ku Ulaya, limene sililemekeza ufulu umene munthu ali nawo wokana kulowa usilikali

Komatu dziko la Turkey lili m’Bungwe la Mayiko a ku Ulaya ndipo linavomereza kuti lizitsatira malamulo ndi mfundo zonse zimene zili m’Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Malinga ndi malamulo amene mayiko a m’bungweli anagwirizana, boma la Turkey lili ndi udindo wotsatira mfundo zimene zili m’chigamulo chomwe chinaperekedwa ndi Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya, pa mlandu wa a Bayatyan ndi Dziko la Armenia. Koma dziko la Turkey lakana kutsatira mfundo zimenezi. Izi zachititsa kuti anthu amene akukana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira azizunzidwa kwambiri.

Kwa zaka zoposa 10 zapitazi, amuna a Mboni za Yehova ku Turkey omwe akhala akulembera makalata akuluakulu a dzikolo popempha kuti ufulu wawo wokana kulowa usilikali uzilemekezedwa, ndi okwana 55. Koma bomalo lakhala likukana pempho limeneli. Izi zachititsa kuti a Mboniwo aziimbidwa milandu kukhoti, azilamulidwa kuti apereke chindapusa cha ndalama zambirimbiri, komanso ena azimangidwa. Panopa, pali amuna achinyamata 15 a Mboni za Yehova ku Turkey amene akuimbidwa milandu mobwerezabwereza chifukwa chokana kulowa usilikali.

‘Ndiyenera Kutsatira Zimene Ndimaphunzira M’Baibulo’

“Ndikukhulupirira kuti boma silikuyenera kundikakamiza kuti ndichite zinthu zotsutsana ndi mfundo za m’Baibulo zimene ndimayendera komanso mawu a Mulungu amene ali pa Yesaya 2:4, omwe ndikukhulupirira kuti ndikuyenera kuwamvera.” Vesi la m’Baibulo lodziwika bwino limeneli, linalembedwa pamwala umene uli kutsogolo kwa maofesi omwe ndi likulu la bungwe la United Nations mumzinda New York City. Vesili limasonyeza kuti anthu sayenera kumenya nkhondo ndipo akufunika ‘kusula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndipo sakuyenera kuphunziranso nkhondo.’ Amene analankhula mawuwa ndi mnyamata wina yemwe pa nthawiyo anali ndi zaka 25, dzina lake Feti Demirtaş, wa m’dziko la Turkey. Iye ananena mawuwa pofotokoza chifukwa chake analolera kutsekeredwa m’ndende m’malo molowa usilikali. Feti ndi wa Mboni za Yehova ndipo amakhulupirira kwambiri kuti akuyenera kumatsatira mfundo zimene amaphunzira m’Baibulo. Zimenezi zachititsa kuti Feti aonekere m’khoti nthawi zokwanira 10, pa milandu imene boma likumuzenga, ndipo wakhala m’ndende kwa zaka pafupifupi ziwiri.

Pa nthawi yoyamba imene Feti anamangidwa, mkulu wa asilikali anamulamula kuti avale yunifomu ya asilikali, koma mnyamatayu anakana potsatira mfundo zimene amaphunzira m’Baibulo. Kenako mkulu wa asilikaliyo anam’tenga Feti n’kumuimika kutsogolo kwa anthu 400, n’kumulamulanso kuti avale yunifomu ya asilikali ija. Koma Feti anakananso. Pa nthawi yoyamba imene Feti anamangidwayi, asilikali olondera ndende anamunyoza, anamumenya m’mutu, m’mapewa, m’miyendo komanso anamupatsa makofi.

Feti anamangidwa ka chi 5 mu April 2006. Pa nthawiyi, asilikali olondera ndende anamulanda zovala zake zonse n’kungomusiyira zamkati zokha. Asilikaliwo anachita izi n’cholinga choti Feti asowe chovala mpaka afike povala yunifomu ya usilikali. Koma mnyamatayu anakanabe kuvala yunifomuyo. Asilikaliwo ataona izi, anamutenga n’kukamuika kumalo ena olangira anthu, ndipo anakhalako kwa masiku 4. Kumalo amenewa, usiku wonse Feti ankamumanga manja ndi unyolo n’kumumangirira kuchitsulo cha bedi lake. Masana, ankamumangirira kuchitsulo china chomwe chinali m’mbali mwa khoma. Feti anati: “Ndinali ndi mantha kwabasi chifukwa sindinkadziwa kuti kugwanji kunja kukada ngakhalenso kukacha. Ndinkalephera kugona chifukwa cha mantha poganizira nkhanza zimene angandichitire. Ngakhale kuti ndinkazunzidwa koopsa, sindinalole kuchita zinthu zosemphana ndi mfundo za m’Baibulo zimene ndimakhulupirira.”

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Likuunikanso Nkhani Yokhudza Kukana Kulowa Usilikali

Mu 2007, Feti Demirtaş analembera kalata Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya kuti limuthandize pa zimene boma la Turkey linachita. Bomali linamuphwanyira ufulu wake n’kumutumiza kundende chifukwa choti anakana kulowa usilikali. Pa January 17, 2012, khotili linaweruza nkhaniyi mokomera Feti. Khotili linagamula kuti boma la Turkey linalakwa pozunza mwankhanza kwambiri komanso pophwanya ufulu wa mnyamatayu. Komanso khotili linanena motsindika mfundo yakuti munthu aliyense ali ndi ufulu wokana kulowa usilikali potsatira mfundo zachipembedzo zimene amakhulupirira. Khotili linanena kuti ufulu umenewu umatetezedwa ndi mfundo zimene zili mu Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya. a

Malinga ndi chigamulo chomveka bwino chimene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linapereka, Feti akuyembekezera kuti akuluakulu a boma la Turkey asiya kumuzunza. Ndipotu boma la Turkey lamupatsa kale ndalama za chipukuta misozi zokwana mayuro 20,000. Izi zachitika potsatira zimene khotili linalamula. Komabe patangotha miyezi 4 yokha kuchokera pamene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linapereka chigamulo chake pa mlandu wa Feti Demirtaş ndi Boma la Turkey, khoti la asilikali ku Turkey linagamulanso kuti Feti amangidwe kwa miyezi awiri ndi hafu chifukwa chokana kulowa usilikali. Panopa Feti wachita apilo mlanduwu ndipo ayembekezera kuti amve zimene khoti la asilikalilo linganene pa nkhaniyi.

Nthambi ya Bungwe la UN Yoona za Ufulu Wachibadwidwe Ikugwirizana ndi Zoti Munthu Ali ndi Ufulu Wokana Kulowa Usilikali

Boma la Turkey lakhala likunyozera zimene linalamulidwa ndi nthambi ya bungwe la UN, Yoona za Ufulu Wachibadwidwe. Mwachitsanzo, mu 2008 anthu awiri a Mboni za Yehova, omwe ndi a Cenk Atasoy ndi a Arda Sarkut, anadandaula ku nthambi ya bungwe la UN imeneyi pa zimene akuluakulu a boma la Turkey akuwachitira. Iwo anadandaula kuti boma lakhala likuwaimba milandu mobwerezabwereza chifukwa choti anakana kulowa usilikali. Nthambi ya bungwe la UN Yoona za Ufulu Wachibadwidwe inatulutsa chigamulo chake chokhudza nkhaniyi pa March 29, 2012. Mawu ena amene anali m’chigamulocho anali akuti “amunawa akukana kulowa usilikali chifukwa cha mfundo zachipembedzo zimene amakhulupirira,” ndipo “zimene zinachitika powaimba mlandu komanso kuwamanga n’zowaphwanyira ufulu wawo wotsatira zimene amakhulupirira. Zimene akuluakulu a boma la Turkey achita zikusemphana ndi ndime 1 ya mutu 10 wa malamulo a mu [Pangano la Dziko lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale].”

Kodi akuluakulu a boma la Turkey akuchita zotani pa nkhani yotsatira chigamulo chomveka bwinochi? Iwo akufunabe kuti anthu awiri a Mboniwa azigwira ntchito zausilikali miyezi 4 iliyonse b ndipo akapanda kutero, azimangidwa kapena kulipiritsidwa ndalama zankhaninkhani za chindapusa.

A Mboni za Yehova ku Turkey ndi otsimikiza ndi mtima wonse kuti apitiriza kutsatira lamulo la m’Baibulo loti azikonda anthu anzawo. Wa Mboni aliyense ayenera kusankha yekha zochita akaitanidwa ndi akuluakulu a boma kuti akagwire ntchito zausilikali. Feti Demirtaş pamodzi ndi anthu ena a Mboni atsimikiza ndi mtima wonse kuti sanganyamule zida chifukwa kuchita zimenezo n’kosagwirizana ndi chikumbumtima chawo komanso n’kuphwanya malamulo a m’Baibulo.

Achinyamata amenewa ali ndi chikhulupiriro chakuti boma lawo lilemekeza zimene lauzidwa kuti lichite ndi a khoti komanso mabungwe oona za ufulu. Nalonso Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya pamodzi ndi nthambi ya bungwe la UN Yoona za Ufulu Wachibadwidwe, akuyembekezera kuti boma la Turkey litsatira zigamulo zawo, zomwe zingachititse kuti dzikoli lizilemekeza ufulu umene anthu ali nawo wokana kolowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Panopa dziko la Turkey silikutsatira mfundo za Bungwe la Mayiko a ku Ulaya chifukwa choti silinayambebe kulemekeza ufulu wofunika kwambiri umene munthu aliyense ali nawo, wokana kulowa usilikali potsatira zimene munthuyo amakhulupirira.

a Aka sikoyamba kuti Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya lipereke chigamulo chotsutsa zimene boma la Turkey likuchita pa nkhani yosalemekeza ufulu umene munthu ali nawo, wokana kulowa usilikali. Mu November 2011, khotili linagamula mlandu wina mokomera munthu wina wa Mboni za Yehova wa ku Turkey, dzina lake Yunus Erçep. Munthuyu anamangidwa maulendo 41 pa nthawi ya zaka 14, chifukwa chokana kulowa usilikali.

b Chaposachedwapa, boma lasintha zinthu n’cholinga choti anthu aziitanidwa kukagwira ntchito za usilikali miyezi itatu iliyonse.