Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Myrat Orazgeldiyev

SEPTEMBER 7, 2020
TURKMENISTAN

Khoti la ku Turkmenistan Lamanga M’bale Myrat Orazgeldiyev Chifukwa Chokana Usilikali

Khoti la ku Turkmenistan Lamanga M’bale Myrat Orazgeldiyev Chifukwa Chokana Usilikali

Chigamulo

Pa 3 September 2020, khoti la m’boma la Vekilbazar M’chigawo cha Mary linagamula kuti M’bale Myrat Orazgeldiyev akakhale kundende chaka chimodzi chifukwa chokana usilikali potengera zimene amakhulupirira. M’baleyu achita apilo chigamulochi.

Zokhudza M’baleyu

Myrat Orazgeldiyev

  • Chaka Chobadwa: 2002 (Mumzinda wa Mary)

  • Mbiri yake: Ankagwira ntchito yoperekera zakudya kuti azipeza ndalama zothandizira banja lake. Mayi ake anamuphunzitsa za Yehova. Amakonda kuchita masewera osiyanasiyana komanso kulemba nyimbo

Mlandu Wake

Ofesi yolemba anthu usilikali inaitana M’bale Orazgeldiyev kuti akayambe usilikali mu June 2020. Apa n’kuti patatha mwezi umodzi atakwanitsa zaka 18. M’bale Orazgeldiyev anafotokoza zifukwa zimene sangagwirire ntchito ya usilikali ndipo anapempha kuti apatsidwe ntchito ina yosakhudzana ndi usilikali.

Pa 1 July 2020, anthu atatu ochokera ku ofesi yolemba anthu usilikali anapita kunyumba kwa M’bale Orazgeldiyev kuti akamutenge. Koma iye anakana kupita nawo. Tsiku lomwelo anapita naye kuchipatala kuti akamuyeze ndipo anapeza kuti m’baleyu akhoza kukwanitsa kugwira ntchito ya usilikali.

Pa 14 July 2020, loya woimira boma pamlanduwu anaitana M’bale Oragzgeldiyev kuti akamufunse mafunso ena. Mwezi wotsatira m’baleyu anauzidwa kuti wapezeka ndi mlandu ndipo panakonzedwa tsiku loti mlanduwu ukazengedwe.

Tikupemphera kuti Yehova apitirize kuthandiza M’bale Orazgeldiyev komanso abale ena achinyamata 10 omwe ali m’ndende kuti akhale olimba mtima ndiponso amphamvu. Tili ndi chikhulupiriro chakuti Yehova ayankha mapemphero athu.—Salimo 31:24.