Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Ihlosbek Rozmetov

JANUARY 22, 2021
TURKMENISTAN

M’bale Ihlosbek Rozmetov Wagamulidwa Kachiwiri Kuti Akakhale Kundende Atakana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

M’bale Ihlosbek Rozmetov Wagamulidwa Kachiwiri Kuti Akakhale Kundende Atakana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Chigamulo

Pa 19 January 2021, khoti lina laling’ono ku Turkmenistan linagamula kuti M’bale Ihlosbek Rozmetov ndi wolakwa. Khotili linagamula kuti M’baleyu akakhale kundende ya chitetezo champhamvu kwambiri kwa zaka ziwiri atakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Aka n’kachiwiri kuti M’baleyu aikidwe m’ndende chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira.

Zokhudza M’baleyu

Ihlosbek Rozmetov

  • Chaka chobadwa: 1997 (ku Andalib)

  • Mbiri yake: Anabadwa ana awiri m’banja lawo ndipo ali ndi zaka 10 anayamba kugwira ntchito akangoweruka kusukulu n’cholinga choti azithandiza banja lawo. Amakonda kuchita masewera olimbitsa thupi, kuwerenga mabuku komanso kumvetsera nyimbo. Mayi ake anayamba kuphunzira Baibulo mu 2010 ndipo mu 2011 nayenso anayamba kuphunzira Baibulo

Mlandu Wake

Pa 11 July 2018, M’bale Ihlosbek Rozmetov anagamulidwa kuti akagwire ukaidi kwa chaka chimodzi kundende yozunzirako anthu ku Seydi chifukwa choti anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Pa nthawiyi n’kuti ali ndi zaka 20. M’baleyu anatulutsidwa m’ndende atamaliza kugwira ukaidi wake kwa chaka chimodzi. Malinga ndi malamulo a dziko la Turkmenistan, munthu amene wakana kulowa usilikali potengera zimene amakhulupirira amatha kuimbidwa mlandu kawiri.

Pa 25 November 2020, M’bale Rozmetov anauzidwanso kuti alowe usilikali. Iye anafotokoza mwaulemu zimene amakhulupirira monga Mkhristu. Komabe, akuluakulu a boma anayamba kumuzenga mlandu wina ndipo pa nthawiyi anagamulidwa kuti akakhale m’ndende nthawi yaitali kuposa poyamba paja chifukwa kanali kachiwiri kuimbidwa mlandu pa nkhani yomweyo.

M’bale Rozmetov akufotokoza kuti “anavutika kwambiri” nthawi yoyamba imene anakhala m’ndende. Koma mavesi a m’Baibulo amene anawerenga n’kuloweza asanapite kundende anamuthandiza kwambiri pa nthawi yovutayi. Lemba limene linamuthandiza kwambiri ndi la Afilipi 4:6, 7. Mavesi awiriwa anamuthandiza kuti ‘asamade nkhawa ndi kanthu kalikonse,’ azipempherera “mtendere wa Mulungu” komanso kuti akhale wodekha pa nthawi yovutayi. M’bale Rozmetov anati: “Pa nthawi yovutayi ndinkapemphera kwa Yehova pafupipafupi ndipo ndinkamva kuti ali nane pafupi.”

Tikukhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova apitiriza kulimbitsa M’bale Rozmetov ndi onse amene amayembekezera mwa Iye.—Yesaya 40:29-31.