Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Maksat Jumadurdyyev

JANUARY 28, 2021
TURKMENISTAN

M’bale Maksat Jumadurdyyev Wamangidwa Kachiwiri Atakana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

M’bale Maksat Jumadurdyyev Wamangidwa Kachiwiri Atakana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Chigamulo

Pa 18 January 2021, Khoti la ku Turkmenistan linagamula kuti M’bale Maksat Jumadurdyyev ndi wolakwa. M’baleyu anauzidwa kuti akakhale kundende zaka ziwiri atakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

Zokhudza M’baleyu

Maksat Jumadurdyyev

  • Chaka chobadwa: 2000 (Ku Seydi, m’Chigawo cha Lebap)

  • Mbiri yake: Ali ndi azichemwali ake awiri. Amakonda kuphunzira. Amakonda kuchita masewera olimbitsa thupi. Ali ndi luso lojambula ndi kukongoletsa zithunzi. M’dera lawo amadziwika monga munthu wodzichepetsa, wochita zinthu moona mtima komanso wolimbikira kugwira ntchito

    Anayamba kuphunzira Baibulo mu 2018. Anabatizidwa mu 2019. M’banja mwawo alimo yekha wa Mboni za Yehova.

Mlandu Wake

M’bale Maksat Jumadurdyyev anali atakhala m’ndende kwa chaka chimodzi chifukwa chokana kulowa usilikali. Pa 17 July 2019 anatulutsidwa m’ndende. Malinga ndi lamulo lomwe linakhazikitsa m’dziko la Turkmenistan, anthu amene akana kulowa usilikali chifukwa cha chikhulupiriro chawo amaimbidwa mlandu kawiri. Izi zinachititsa kuti mu March 2020 m’baleyu auzidwenso kuti akalowe usilikali. M’bale Jumadurdyyev analemba kalata yofotokoza kuti sakufuna kulowa usilikali ngakhale kuti ankadziwa kuti atha kupita kundende kachiwiri.

Apolisi anayamba kufunsa mafunso M’bale Jumadurdyyev ndipo anachita zimenezi maulendo ambirimbiri komanso anamukakamiza kuti apite kuchipatala n’cholinga choti madokotala akamuyeze ngati ali ndi matenda kapena ayi. Kenako pa 30 December 2020, apolisiwo anauza m’baleyu kuti amupeza ndi mlandu wina. Apolisiwo analandanso m’baleyu pasipoti.

M’bale Jumadurdyyev anavutika kwambiri pa nthawi imene ankaimbidwa mlandu komanso ataikidwa m’ndende koyamba. Iye akunena kuti: “Nditapita kundende mu 2018, ndinavutika kwambiri kusiyana ndi makolo anga. . . . Popeza kuti makolo anga si a Mboni za Yehova, anandiuza kuti ndikakana kulowa usilikali iwowo sandithandiza pa zomwe ndasankhazo.”

M’baleyu akufotokoza kuti: “Mawu a pa Maliko 10:29, 30, anandithandiza kwambiri kupirira nditasiyana ndi makolo komanso anzanga. Yesu ananena kuti tikalolera kusiya zinthu ndi anthu omwe timawakonda chifukwa cha iyeyo komanso uthenga wabwino, tidzapeza zochuluka kuwirikiza maulendo 100.”

Pa nthawi yonse yomwe M’bale Jumadurdyyev anali m’ndende, ankaona mmene Yehova ankayankhira mwansanga mapemphero ake komanso kumuthandiza kupirira mavuto. Nthawi zambiri m’baleyu ankakumbukira mawu a m’lemba la Yoswa 1:9 lomwe limati: “Ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Usachite mantha kapena kuopa, pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.”

M’bale Jumadurdyyev asanayambe kuzengedwa mlandu kachiwiri ananena kuti ndi wotsimikiza mtima kumvera chikumbumtima chake chophunzitsidwa bwino Baibulo. Iye anati: “Ngati ndingapite kundende kachiwiri, sindikukayikira kuti Yehova andithandiza zivute zitani. Malangizo omwe ali pa Afilipi 4:6,7 amandithandiza kukhala wolimba mtima komanso kuchita zinthu modekha.”

Tikupitiriza kupempherera M’bale wathu Jumadurdyyev komanso abale ena achinyamata amene akufunitsitsa ndi mtima wonse kukhala kumbali ya ulamuliro wa Yehova. Tikukhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova adalitsa abale athu onse omwe ali m’ndende chifukwa cha kukhulupirika kwawo.—Chivumbulutso 2:10.