Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 3, 2020
TURKMENISTAN

M’bale Petrosov Watulutsidwa M’ndende Pambuyo Pogwira Ukaidi kwa Chaka Chimodzi ku Turkmenistan

M’bale Petrosov Watulutsidwa M’ndende Pambuyo Pogwira Ukaidi kwa Chaka Chimodzi ku Turkmenistan

M’bale David Petrosov ali ndi zaka 19 ndipo amakhala ku Turkmenistan. Ngakhale kuti sanakwanitse zaka 20, chikhulupiriro chake chinayesedwa kwambiri. Tikutero chifukwa anagwira ukaidi kwa chaka chimodzi chifukwa chokana usilikali potsatira zimene amakhulupirira. Iye anatulutsidwa m’ndende pa 30 September 2020.

M’bale Petrosov anati: “Masiku ena ndili m’ndende ndinkakhala wokhumudwa kwambiri. Koma Yehova ankanditonthoza ndi Mawu ake. Sindinkasiya kupemphera kwa Yehova chifukwa ndinkadziwa kuti iye amamvetsa mmene ndikumvera komanso anali wokonzeka kunditonthoza. Ndinkawerenga mavesi osiyanasiyana pa mavuto amene ndinkakumana nawo, koma nthawi zambiri ndinkakumbukira lemba la Afilipi 4:13.”

M’bale Petrosov anabadwira mumzinda wa Ashgabat womwe ndi likulu la dziko la Turkmenistan. Pamene ankakula anaphunzira kuimba gitala. Iye amakonda kupeka nyimbo, kusewera mpira wamiyendo, kukwera mapiri komanso kusambira kunyanja zakwawoko.

Anaphunzitsidwa Baibulo ndi mnzake wam’kalasi yemwe anali wa Mboni za Yehova ndipo mu 2019 anabatizidwa. Ngakhale kuti abale ake a David si a Mboni, iwo amalemekeza zimene David amakhulupirira zokhudza Mulungu.

Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene anabatizidwa, David anapititsidwa kukhoti chifukwa chokana kulowa usilikali. M’dziko la Turkmenistan mulibe lamulo lolola anthu kugwira ntchito zina m’malo mwa usilikali. Choncho khoti linagamula kuti David akakhale kundende kwa chaka chimodzi.

Pa nthawi imene David anali m’ndende, Yehova anamuthandiza kwambiri. Iye akunena kuti: “Pamene ndinali m’ndende, mayi anga anandiuza za abale ndi alongo omwe sakanatha kudzandiona koma ananditumizira moni wawo. Anandiuza kuti abale ndi alongowa ankandipempherera nthawi zonse. Zimenezi zinandithandiza kuti ndizikhala wosangalala.”

David akudziwa kuti akhoza kuikidwanso pa m’ndandanda woti akalowe usilikali malinga ndi lamulo la dziko la Turkmenistan. Ngati zimenezi zingadzachitikedi, David atha kudzapezekanso ndi mlandu ndipo akhoza kudzauzidwa kuti akakhale kundende kwa nthawi yochulukirapo.

David akunena kuti: “Palibe amene amafuna kubwereranso kundende ndipo inenso sindikufuna. Koma sindikuopa. Ndimapeza mphamvu chifukwa ndimakhulupirira Yehova, abale ndi alongo anga amandilimbikitsa komanso ndimalimbikitsidwa ndi nyimbo zathu za Ufumu.”

Tikukhulupirira kuti Yehova apitiriza kupatsa David mphamvu komanso chikhulupiriro cholimba. Tikupemphereranso abale 10 omwe adakali m’ndende ku Turkmenistan chifukwa chokana usilikali potsatira zimene amakhulupirira. Tikudziwa kuti Yehova amawakonda, kuwakumbukira komanso kuwathandiza.—Salimo 69:33.