Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Ruslan Artykmyradov

JANUARY 11, 2021
TURKMENISTAN

M’bale Ruslan Artykmyradov Atha Kugamulidwa Kachiwiri Kuti Akakhale Kundende Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake

M’bale Ruslan Artykmyradov Atha Kugamulidwa Kachiwiri Kuti Akakhale Kundende Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake

Tsiku Lopereka Chigamulo

Khoti la asilikali ku Turkmenistan posachedwapa * lidzapereka chigamulo chake pa mlandu wokhudza M’bale Ruslan Artykmyradov. Iye atha kugamulidwa kuti akakhale kundende zaka ziwiri chifukwa chokana usilikali potsatira zimene amakhulupirira. M’baleyu wakhala ali m’manja mwa apolisi kuyambira pa 15 December 2020. Aka n’kachiwiri kuti aimbidwe mlandu chifukwa chokana usilikali.

Zokhudza M’baleyu

Ruslan Artykmyradov

  • Chaka chobadwa: 2000 (m’mudzi wa Alpan Gengeshlik)

  • Mbiri yake: Anakulira m’dera lakumudzi. Amagwira ntchito ya umakaniko. Anali mwana wabwino kwambiri kusukulu ndipo amakonda kusewera mpira wamiyendo

    Anaphunzitsidwa Baibulo ndi mayi ake ndipo anayamba kugwiritsa ntchito zomwe ankaphunzirazo pamoyo wake. Anasangalala kwambiri ataona chikondi komanso mgwirizano womwe a Mboni za Yehova amasonyezana ndipo mu 2015 anabatizidwa ali ndi zaka 15. Anakana kulowa usilikali chifukwa choti amakonda kwambiri Yehova Mulungu

Mlandu Wake

Pa 13 August 2018, M’bale Ruslan Artykmyradov anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali. Apa n’kuti ali ndi zaka 18. Pa 12 August 2019 anatulutsidwa m’ndende pambuyo pomaliza kugwira ukaidi kwa chaka chimodzi.

Malinga ndi malamulo a dziko la Turkmenistan, achinyamata amatha kuimbidwa mlandu kawiri chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira. Choncho, mu November 2020, M’bale Artykmyradov anauzidwanso kuti akalowe usilikali.

Apanso M’bale Artykmyradov anakana kulowa usilikali ndipo ankadziwa bwino kuti zimenezi zitha kuchititsa kuti apite kundende kachiwiri. Pa 15 December 2020, M’baleyu anamangidwa ndipo anamusunga m’ndende poyembekezera kuzenga mlandu wake.

M’bale Artykmyradov ndi wotsimikiza kuti akhalabe wokhulupirika kwa Yehova. Malinga ndi zimene zinachitika pa nthawi ya mlandu wake woyamba, iye akufotokoza kuti: “Sindinkachita mantha, ngakhale kuti ndinkadziwa kuti ndikumana ndi mavuto komanso zinthu zopanda chilungamo. Koma sindikanalola kusinthanitsa chimwemwe changa ndiponso ubale wamphamvu womwe ndili nawo ndi Yehova ndi chinthu china chilichonse.”

M’bale Artykmyradov anakhala moyo wovutika m’ndende. Zinthu sizinali bwino ndipo ankazunzidwa. Koma ngakhale zinali choncho, ankatha kuona kuti Yehova akumuthandiza. Iye akunena kuti: “Pa nthawi yomwe ndinali m’ndende, nthawi zambiri ndinkaona kuti Yehova akundithandiza. Mwachitsanzo, ndinkaona kuti Yehova akundithandiza kuti ndisamve ululu winawake akamandimenya. Ndinkangomva ululu koyamba koma kwinako ayi.” Kuonjezera pamenepa chikondi chimene abale ndi alongo ankamusonyeza chinkamulimbikitsa komanso chinathandiza anthu ena omwe anali naye m’ndendemo.

Ngakhale kuti akupitanso kundende kachiwiri, M’bale Artykmyradov ali ndi chikhulupiriro kuti Yehova amuthandiza ndipo akufotokoza kuti: “Ndili ndi chikhulupiriro champhamvu kuti Yehova adzandifupa. . . . Munthu ukakhala ndi chiyembekezo champhamvu, umakhala ndi chimwemwe chosatha; ukakhala ndi chimwemwe, umakhala ndi mphamvu ndipo umatha kupilira. Ndipo munthu wolimba samagwedezeka.”

Tikusangalala kuona chitsanzo cha M’bale Artykmyradov komanso achinyamata ena olimba mtima amene amapereka umboni woti Yehova amatithandiza kukumana ndi mayesero molimba mtima komanso mosangalala. Tikudziwanso kuti adzalandira mphoto chifukwa chokhalabe okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu.—Aheberi 11:6.

^ Tsiku lenileni lopereka chigamulo nthawi zina silimadziwikiratu.