Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MARCH 20, 2019
TURKMENISTAN

A Bahram Hemdemov Awatulutsa M’ndende

A Bahram Hemdemov Awatulutsa M’ndende

Pa 13 February, 2019, a Bahram Hemdemov a zaka 55 anatulutsidwa m’ndende ya ku Seydi (LB-E/12) ku Turkmenistan, pambuyo pogwira ukaidi wazaka 4. Panopa alinso limodzi ndi akazi awo a Gulzira komanso ana awo 4. Bambo Hemdemov anamangidwa pa 14 March, 2015, chifukwa chochita msonkhano wachipembedzo kunyumba kwawo mumzinda wa Turkmenabad. Ndipo pa 19 May, 2015, khoti la m’boma la Lebap, linagamula kuti a Hemdemov ndi olakwa. Boma la Turkmenistan lakhala likukhululukira akaidi maulendo atatu pafupifupi chaka chilichonse pa nthawi imene bambo Hemdemov anaikidwa m’ndende, koma nthawi iliyonse imene akaidi ena kuphatikizapo a milandu yakupha anthu ankatulutsidwa m’ndende, iwowa sankaikidwa pagululi. Pa 15 August, 2016, bambo Hemdemov anakadandaula ku Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu, ndipo akuyembekezerabe kuti komitiyi iwathandize. A Mboni za Yehova okwana 11 ku Turkmenistan adakali m’ndende chifukwa chokana kulowa usilikali, ngakhale kuti Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu inapereka zigamulo 10 zotsutsa boma la Turkimenistan chifukwa chozunza ndi kutsekera m’ndende anyamata a Mboni amene anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.