Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 10, 2016
TURKMENISTAN

Dziko la Turkmenistan Lakana Kukhululukira a Mboni Omwe Anawamanga

Dziko la Turkmenistan Lakana Kukhululukira a Mboni Omwe Anawamanga

Pa 25 October, 2016 pulezidenti wa dziko la Turkmenistan, anakhululukira akaidi oposa 1,500. Koma pulezidentiyu sanakhululukire a Bahram Hemdemov ndi a Mansur Masharipov omwe ndi a Mboni za Yehova ndipo anamangidwa ndi kutsekeredwa ku ndende ya LBK-12 yomwe ili m’tauni ya Seydi.

A Hemdemov akhala ali m’ndende kuyambira March 2015 ndipo anawamanga chifukwa chochititsa misonkhano yachipembedzo mwamtendere ku nyumba kwawo ku Turkmenabad. Khoti lina ku Turkmenistan linagamula kuti a Hemdemov akhale m’ndende zaka 4 chifukwa chochita zachipembedzo zomwe akuti ndi zosemphana ndi malamulo. A Masharipov, anawamanga ku Ashgabad mu June 2016 pa mlandu wongonamizira ndipo anawagamula kuti akhale m’ndende chaka chimodzi. Achibale awo komanso a Mboni za Yehova padziko lonse ndi okhumudwa kuona kuti anthu awiriwa sanatulutsidwe. Komabe iwo ali ndi chiyembekezo kuti mwina anthuwa adzawaganizira ulendo wina akamadzakhululukira akaidi ena.