Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kerven Kakabayev—waweruzidwa kuti akakhale m’ndende chaka chimodzi chifukwa chokana usilikali

MARCH 28, 2018
TURKMENISTAN

Dziko la Turkmenistan Likukana Kupereka Ufulu Wotsatira Zimene Munthu Amakhulupirira

Dziko la Turkmenistan Likukana Kupereka Ufulu Wotsatira Zimene Munthu Amakhulupirira

Mu January 2018, Arslan Begenjov ndi Kerven Kakabayev anaweruzidwa kuti akakhale m’ndende chaka chimodzi chifukwa chokana usilikali. Anyamatawa ndi a Mboni ndipo anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Ngakhale kuti anavomera kugwira ntchito ina yosakhudza usilikali, boma la Turkmenistan sililemekeza ufulu wa anthu okana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira ndipo sililola kuti anthu agwire ntchito ina m’malo mwa usilikali.

Anamangidwa, Kuweruzidwa Kuti Ndi Olakwa N’kuikidwa M’ndende

Asilikali anamanga Arslan Begenjov pa 2 January ndipo anamuika m’ndende podikira kuti mlandu wake uzengedwe. Pa 17 January, khoti linagamula kuti ndi wolakwa pa mlandu wokana usilikali ndipo linalamula kuti akakhale m’ndende kwa chaka chimodzi. Iye anachita apilo chigamulo chopanda chilungamochi.

Nayenso Kerven Kakabayev anamangidwa mu January ndipo pa 29 January anaweruzidwa kuti akakhale m’ndende chaka chimodzi. Pozenga mlandu wake, khoti silinalole kuti iye afotokoze zigamulo zimene Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu inapereka zokomera anthu okana usilikali. Komanso n’zomvetsa chisoni kuti mwina palibe khoti limene lidzamvetsere apilo yake. Zili choncho chifukwa akuluakulu akundende sanamupatse zikalata za apilo zimene maloya ake anakonza. Choncho sanathe kusaina zikalatazo pa nthawi yoyenera, chifukwa lamulo limanena kuti ziyenera kusainidwa masiku 10 asanakwane kuchokera pa nthawi imene anaweruzidwa.

Kerven Kakabayev akulangidwa kachiwiri chifukwa chokana usilikali. Mu December 2014, makhoti anamulamula kuti kwa zaka ziwiri azipereka ku boma 20 peresenti ya malipiro a kuntchito kwake.

“Likulepherabe Kulemekeza Ufulu wa Anthu Wokana Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira”

Boma la Turkmenistan limanena kuti limalemekeza ufulu wa anthu ake. Koma limakana kulemekeza ufulu wa anthu okana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira ngakhale kuti anthu akulipempha kuti litsatire malamulo okhudza zimenezi apadziko lonse.

Mu 2015 ndi 2016, Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu inapereka zigamulo zotsutsa dziko la Turkmenistan chifukwa cha madandaulo amene inalandira kuchokera kwa a Mboni amene anakana usilikali. Komitiyi inadzudzula dziko la Turkmenistan chifukwa chozunza ndiponso kumanga a Mboni okana usilikali. Mu April 2017, komitiyi inanenanso kuti ikudandaula kuti dziko la Turkmenistan “likulepherabe kulemekeza ufulu wa anthu wokana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira ndipo likupitirizabe kuimba mlandu ndiponso kumanga a Mboni za Yehova amene akana usilikali.” Inapemphanso dzikoli kuti liyambe kulola kuti anthu azigwira ntchito ina m’malo mwa usilikali, lisiye kuimba mlandu anthu okana usilikali ndipo limasule anthu amene ali m’ndende chifukwa cha zimenezi.

Pa zaka zapitazi, boma lasintha zinthu zina zimene limachita pa nkhaniyi. Kuyambira mu December 2014, m’malo momanga a Mboni amene akana usilikali, lakhala likuwalipiritsa 20 peresenti ya malipiro awo kwa chaka chimodzi kapena ziwiri ngati mmene linachitira ndi Kerven Kakabayev. Apo ayi lakhala likupereka chilango china. a Mu February 2015, bomali linamasula wa Mboni womaliza amene anamangidwa chifukwa chokana usilikali. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti pa milandu ya posachedwapa ya Arslan Begenjov ndi Kerven Kakabayev, boma layambiranso kupereka zilango zokhwima ndipo silikulemekeza ufulu wa anthu wokana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

A Mboni Ena Amangidwa pa Zifukwa Zina Zachipembedzo

Kuwonjezera pa kuika Arslan Begenjov ndi Kerven Kakabayev m’ndende, boma likusungabe Bahram Hemdemov m’ndende chifukwa chochita zinthu mogwirizana ndi ufulu wake wa chipembedzo. Iye ndi wa Mboni ndi anamangidwa chifukwa chochita msonkhano wachipembedzo m’nyumba yake ku Turkmenabad. Bamboyo ali ndi ana 4 ndipo wakhala m’ndende kuyambira mu 2015, ngakhale kuti pulezidenti wa Turkmenistan walamula kuti anthu ambiri amasulidwe m’ndende pa zaka ziwiri zapitazi. Boma lamasula akaidi masauzande ambiri mwachifundo koma akunyalanyazabe zimene anthu akupempha zoti Bahram Hemdemov amasulidwe.

A Mboni za Yehova akufunitsitsa kuti Akhristu anzawo ku Turkmenistan amasulidwe. Iwo akufuna kuti boma la Turkmenistan liyambe kulemekeza ufulu wa anthu wa chipembedzo ndiponso wochita zinthu mogwirizana ndi amene amakhulupirira. Angafunenso kuti zinthu zopanda chilungamo zimene zikuchitikira anthu ena zithetsedwe.

a Chilango china chimene amapereka ndi kulamula kuti munthuyo aziyang’aniridwa ndi enaake kwa nthawi inayake.